Kucheza ndi Beatrice Mpinganjira

January 5, 2014 • Nkhani • Written by :

Mpinganjira (ali ndi mpira) kuonetsa luso lake

Mpinganjira (ali ndi mpira) kuonetsa luso lake

Kusewera mpira wamanja ndi kanthu kena. Zimafuna luso kuti zitheke moti anthu angayamike za lusolo. Beatrice Mpinganjira wosewera m’timu ya Tigresses ndi katundu pomasewerowa. Iye amasewera pakati m’timu ya Malawi Queens. Katakweyu amaseweranso basketball. Luso chonchi bwanji? Iye akutsanula zambiri kwa BOBBY KABANGO.

 

Tidziwane…

Ndine woyamba ndi wotsiriza m’banja mwathu.

 

Lusoli lidayamba motani?

Lusoli limaoneka kuti ndi lachibadwa, chifukwa ndidayamba ndili wachichepere umo mudali musitandede 7 ku St Anthony ku Zomba. Koma amandikaniza kuti ndisewerere timu yathu ponena kuti ndidali wa mng’ono. Nditafika sitandede 8 adandiloleza. Apa ndidayamba kusewerera matimu awiri ndi ya Admarc Tigress Youth.

 

Zidatani utamaliza pulaimale?

Ndidapita ku Joyce Banda Foundation. Uko ndimasewera timu ya sukuluyo komanso ya Admarc Tigress yaikulu. Panthawiyi ndimasewera ngati wotchinga m’mbali komanso ngati wotchinga pagolo. Ndili fomu 2 adayamba kunditenga kuti ndikasewere timu yosaposa zaka 21 ya dziko lino.

 

Umachoka kusukulu zalusoli zili pati?

Tisadachoke kusukuluko ndidasewera nawonso mumpikisano wa Cosana womwe udachitikira ku Youth Centre mumzinda wa Blantyre. M’gulu lathu tidatsilizira kumapeto komabe zidasewera bwino chifukwa tidasiyana ndizigoli zochepa ndi Botswana. Kuchoka kusukuluko ndidachita maphunziro aukachenjede a Electronics mpaka level 3. Apo ndidali nditatengedwa kukasewera timu yaikulu mumpikisano wapadziko lonse ku New Zealand. Ndachita maphunziro a zamalonda mpaka kupeza diploma, pano ndikuchita maphunziro a zamasewero.

 

Wasewera mipikisano ingati?

Ndasewera mipikisano 12 m’timu yaikulu yokha momwenso ndasewera magemu 42. Dziwaninso kuti ndimasewera basketball. Timu yanga ndi Netters. Ndinadalitsidwa ndi luso, kumvetsetsa malamulo ake ndiye chinsinsi. Basketball imafanana ndi netball kungoti basketball timanjanjitsa mpira.

 

Umagomera wosewera uti? Nanga ndi ziti umakonda kupatula masewerowa?

Ndimagomera Ellen Chiboko wa Tigresses, nzeru zake posewera zimandidabwitsa. Ndimakonda kuvina, kucheza. Pa chakudya ndimakonda nsima ya nyama ya ng’ombe, kunditero ndiye kumtimaku kuti mbeee!

All views expressed in the comments of users of www.mwnation.com are independent. They are not a reflection of the views of Nation Publications Limited (NPL) nor are they endorsed by NPL. This is a forum provided by NPL to make good on it's corporate slogan of Making freedom of expression a reality.

Comments are closed.

« »