‘Kudali ku Nanzikambe’

August 11, 2013 • Nkhani • Written by :

Nkhwachi ndi Eunice akukwatitsa lero

Nkhwachi ndi Eunice akukwatitsa lero

Si filimu kapena nthabwala, izi ndi zenizeni. Nkhwachi Mhango mkulu wa gulu la zachikhalidwe la Culture and Development Organization Ubuntu Lab akumangitsa woyera ndi Eunice Kadzuwa woimba m’gulu la Mibawa lero lino.

Zonse zikuchitikira ku Tina’s Garden ku Namiwawa pomwe kusangalala kuchitikire ku mpingo wa Word Alive mumzinda wa Blantyre.

Izi zili choncho, awiriwa ali ndi mbiri ya momwe adakumanirana. Nkhwachi akuti wakhala akuponyerana maso ndi Eunice pamene onsewa amagwira ku Nanzikambe. Ntchito ili apo koma awiriwa amaonerana ndi diso lofiira kuti tsiku lina padzachitika kanthu.

Kugwa kwa mawu komanso kutoledwa kwa mawuwo ndiye akuti zachitika chaka chathachi aliyense atazizidwa ndi maonekedwe komanso khalidwe la mnzake.

“Zenizeni zidayamba kuoneka pamene Eunice adali ku Germany ine ndili ku Tanzania. Timacheza kwambiri ndipo kachezedweko kadachititsa kuti zenizeni ziyambe kuchitika,” akusimba mnyamata wa tindevu tosisitikayu.

Iye akuti machezawo pena adali oseketsa komabe amakoma awiriwa akamachezerana kuti timakumanidwe awo ayambe. “Zidatenga pafupifupi miyezi 6 kuti zenizeni ziyambike.”

Kulumikizana kwawo akuti kudali kwa ndii zomwe zidawapatsa chikhulupiriro kuti tsiku lina adzapanga zenizeni.

Nkhwachi wachisanu kubadwa m’banja la ana 8 amachokera m’mudzi mwa Khata kwa T/A Mlowe m’boma la Rumphi.

Eunice womaliza kubadwa m’banja la ana 8 amachokera m’mudzi mwa Chimphamba kwa T/A Nankumba m’boma la Mangochi.

“Zimafunika kuti munthu utsimikize wekha ndipo uzindikire za chomwe ukufuna. Osachita zomwe ena akufuna koma chita zomwe watsimikizika kuti ungathe,” adalangiza Eunice.

All views expressed in the comments of users of www.mwnation.com are independent. They are not a reflection of the views of Nation Publications Limited (NPL) nor are they endorsed by NPL. This is a forum provided by NPL to make good on it's corporate slogan of Making freedom of expression a reality.

Comments are closed.

« »