Nkhani

Kudziwa za m’thupi; kukonza tsogolo

Listen to this article

Sabata yatha inapatulidwa ndi boma pankhani yoyezetsa magazi kuti anthu adziwe ngati ali ndi kachirombo koyambitsa Edzi ka HIV. Mutu wa ntchitoyi chaka chino unali ‘Yezetsani Magazi kuti Mukonze Tsogolo’ ndipo boma linalinga kuti lifikire anthu 250 000.

Pachithunzipa mukuona Mofolo Masulani wa zaka 32 yemwe amagwira ntchito yokonza panja ku Mandala mu mzinda wa Blantyre. Iye anatulukuka m’kachipinda koyezetsera magazi kumsika wa Blantyre ali mweee kusekerera.

“Ndadziwa m’mene ndiliri ndipo tsopano ndikwanitsadi kukonza tsogolo langa,” iye anabwekera. Mkuluyu anati ali pabanja komanso ali ndi ana atatu ndipo aka kanali koyamba kuyezetsa magazi.

Masulani amachokera ku Matindi m’dera la Lunzu, makamaka m’mudzi mwa Jamusoni kwa T/A Kapeni ku Blantyre.

Wogwrizira udindo woyendetsa ntchito zolimbana ndi HIV Edzi m’bomali, Rosemary Ngaiyaye, anati ntchitoyi inayenda bwino ngakhale zipangizo zina zinafika mochedwerapo kapena mochepera pa loto la ofesi yake.

Related Articles

Back to top button