Kukuza ziwalo kwabooka

Masiku ano ukatsegula wailesi kapena nyuzipepala ngakhalenso poyenda mphepepete mwa msewu ngakhalenso m’malo modikirira mabasi, uthenga omwe watenga malo ndi wa mankhwala okuza ziwalo.

Uthengawu umafotokoza kuti asing’anga ali ndi mankhwala okuza zida za abambo, mbina za amayi komanso kuonjezera mphamvu kuchipinda koma boma ngakhalenso bungwe loona za mankhwala sadabwere poyera kunena maganizo awo pankhaniyo.

Mbewe: Zimafunika osalakwitsa

Pomwe ena ali ndi nkhawa kuti mwina mankhwala oterewa angayambitse mavuto ena m’thupi, unduna wa zaumoyo wati palibe munthu yemwe adadandaulapo kuti wavulala ndi mankhwalawa koma wanenetsa kuti izi sizikutanthauza kuti mankhwalawa alibe vuto.

Mneneri wa unduna wa zaumoyo Joshua Malango wati undunawu ukukonza ndondomeko zoyendetsera mankhwala a zitsamba chifukwa lamulo lomwe lilipo la 1988 ndime 15 limangokamba za kayendetsedwe ka mankhwala achizungu basi.

“Mankhwala azitsamba sadayezedwe kuti tidziwe ubwino kapena kuipa kwake koma pozindikira kuti akhozanso kukhala oopsa ngati mankhwala ena onse, tapanga ndondomeko zomwe zikudikira kuti nduna ivomereze basi,” adatero Malango.

Iye adati nduna ikadzangovomereza ndondomekoyi, unduna udzakhala ndi mphamvu zokakamiza onse ochita za zitsamba kuti azikalembetsa mankhwala awo ndi kufotokoza kagwiridwe ntchito kake.

Mmodzi mwa akadaulo

pa nkhani za zitsamba Mustafu Mbewe akuti mankhwalawa alibe vuto lililonse pokhapokha munthu akalakwitsa machitidwe ake mpomwe zimatembenuka ndipo zotsatira zake zimakhala zoopsa.

Mbewe wati pokuza mbina, munthu amayenera kukhalira mafuwa ofunda komanso ofanana kuopa kuti mbinayo ingapotoke pokula ndipo mankhwala ake amachita akumwa, kutema mphini ndi kusina.

Pa chida cha abambo, Mbewe adati nsinjiro yaikulu ndi mvunguti chifukwa munthu amasankha yekha kakulidwe potengera milingo ya mbvunguti yomwe opanga mankhwalayo ali nayo.

Iye adati ngozi yaikulu yagona pogwiritsa ntchito mvunguti omwe udagona pakugwa kapena tsinde lake silidadulidwe bwino atatengako gawo lofunikalo.

“Podula mvunguti, umayenera ulase pansi ndi nsonga chifukwa ukangogwa chogona, chida chimakula koma chimakhala chopanda ntchito ndipo munthu amakhala osabereka chifukwa kuchipinda nako sapanga kanthu.

“Vuto lina, ngati tsinde la mvunguti omwe mwagwiritsa ntchito silidadulidwe, likamakula chidanso chimangokulirakulira mpaka munthu kuyamba kusowa mtendere. Nkhani yaikulu yagona pa ukadaulo wa opanga mankhwalayo,” adatero Mbewe.

Iye adati mankhwalawo akakonzedwa, amasakanizidwa ndi mtengo wina otchedwa mkhazika omwe umapangitsa kuti chidacho chikakula chikhazikike pamlingo omwewo osabwereranso.

Kusiyana ndi mankhwala okuza mbina, iye adati mankhwala okuza chida ali ndi mtsilikulo wake omwe munthu amatha kukatenga akatopa ndi katundu olemetsayo ndipo amabwerera mchilengedwe.

“A amunawa aliko bwino chifukwa munthu akatopa, yekha amatha kubwera ndiye pali mankhwala omwe timasakaniza limodzi ndi mtenthanyerere nkumupatsa. Akatero, chida chake chimabwerera bwinobwino,” adatero Mbewe.

Iye adati abambo ena amakhala opanda mphamvu kuchipinda ndipo izi zikhonza kusokoneza banja kotero palinso mankhwala ena omwe amamupangira munthu otere kuti awonjezere mphamvu zachilengedwe zomwe zikufookazo. n

Share This Post