Chichewa

Kulandira mwana ndi ‘nkanulo’

Listen to this article

Zikhulupiriro zina ukamva, mutu wake weniweni sowe. Pali zambiri zomwe makolo amakhulupilira paumoyo wa munthu kuyambira kubadwa mpaka kumwalira. Anthu ena akuti amakhulupirira kuti mwana akabadwa, pamafunika mwambo wa ‘nkanulo’ ati kusonyeza kuti mwanayo walandiridwadi pakati pa abale. STEVEN PEMBAMOYO adacheza ndi mayi Miriam Chongwe a kwa mfumu yaikulu (T/A) Maganga m’boma la Salima yemwe akufotokoza zambiri za mwambowu.

Mayi Chongwe (kumanja) kulongosola za mwambo wa nkanulo
Mayi Chongwe (kumanja) kulongosola za mwambo wa nkanulo

Mayi, ndati ndicheze nanu pa mwambo wa ‘nkanulo’. Mwambowu ndi wotani?

Uwu ndi mwambo womwe umatsatidwa mwana akabadwa kusonyeza kuti abale ndi anthu pamudzipo amulandira ndipo ndi mmodzi wa iwo. Izi zimatanthauza kuti ndi mfulu kukhala ndi malo monga muja zikhalira ndi malo a banja chifukwa munthu wongobwera amavutika kupeza malo chifukwa palibe mizu yake yomwe angalondoloze.

Mwambowu umayenda bwanji?

Sikuti anthu amachita kusonkhana ngati momwe miyambo ina imakhalira, ayi. Chomwe chimachitika nchakuti mwana akabadwa, chinthu choyambirira n’kudziwitsa abale, makamaka amalume ake kapena azakhali, omwe amakanena kwa amfumu kenako anthu amamasuka kupita kukaona mwanayo ndi kumupititsira mphatso ngati ali nazo.

Mukati chinthu choyambirira mukutanthauzanji poti azaumoyo amati mwana akangobadwa, pompo ayamwe?

Zimenezo n’zoona koma apa tikukamba za mwambo. Umu ndimo makolo kalelo ankakhulupirira zinthu zisadayambe kusintha. Masiku ano miyambo yambiri ikutha pang’onopang’ono chifukwa cha maphunziro, anthu adayamba kuzindikira kuti miyambo ina imaononga mmalo mokonza zinthu.

Tsopano mukati ‘nkanulo’ timadziwa tanthauzo lokanula koma apapa pali mgwirizano wanji ndi mwambo?

Eya, ndimayembekezera funso limenelo. Kumbukani kuti ndati chimakhala chinthu choyambirira mwana akangobadwa ndiye kukanulako n’kutsegula mwanayo kukamwa kuti akhoza kuyamwa chifukwa walandiridwa pakati pa mudzi ndi banja lomwe wabadwiralo.

Inu mudachitapo mwambo umenewu?

M’zaka za mmbuyomo nditangokwatiwa kumene koma kenako ndidazindikira kuti n’kulakwa chifukwa chimakhala chilango kwa mwana. Mwachitsanzo, kumatheka kuti panthawi yomwe mwana wabadwa, palibe mayendedwe achangu malingana nkuti nthawiyo mauthenga amachita kukaperekedwa pakamwa kapena pakalata, foni kudalibe nthawi imeneyo ndiye mudikire munthu ayende kukapereka uthenga kuno mwana ali ndi njala.

Koma madotolo ndi anamwino amadziwa kuti izi zikuchitika?

Sindikudziwa koma zimachitika kwambiri chifukwa chochirira kwa azamba m’midzi. Mwina ndinene kuti kukhwefula ntchito za azamba am’midzi kudathandiza nawo kuchepetsa mwambo umenewu. Sindikukhulupirira kuti dotolo kapena namwino angalekerere izi zikuchitika.

Pano zinthu zili motani?

Panopa zinthu zili bwino chifukwa ndi maphunziro a zauchembere wabwino, anthu tidatsekuka m’maso. Mwina pena ndi pena zikhoza kumachitikabe poti uthenga umafika mosiyanasiyana koma nkhani yaikulu ndi yoti anthu ambiri adatsekuka m’maso chifukwa olo zokachirira kwa azamba am’midzi zidachepa.

Langizo lanu kwa amayi pankhani yokhudza mwambowu n’lotani?

Kwanga n’kuwalimbikitsa kuti miyambo inayi njofunika kuiganizira bwino. Uchembere si chinthu chamasewera, ayi, ngowawa. Ndiye munthu wanzeru sangalole kuti aziona mwana wake akulira chifukwa cha njala chifukwa choti akudikira kuti uthenga ukafike kumudzi kuti kuli mwana. Mwana wobereka wekha sungaponyere munthu wina ameneyo, ndi wako ndithu basi. Chofunika n’kutsatira malangizo a zaumoyo pa zakayamwitsidwe koyenera. n

Related Articles

Back to top button