Kuli zionetsero pa 13 December

Lachitatu pa 13 December kukhala ali ndi mwana agwiritse m’zigawo zonse zitatu za dziko lino pamene bungwe la mipingo la Public Affairs Committee (PAC) litsogolere zionetsero.

Izitu ndi zionetsero zokakamiza boma kuti libweretse mabilo okhudza za chisankho mu Nyumba ya Malamulo.

Chilima (R) adawerenga kalata

Mabilowo, mwa zina, akukamba kuti mtsogoleri wa dziko azisankhidwa ndi mavoti oposa 50 peresenti.

Sinodi ya mpingo wa CCAP ku Livingstonia ndi sukulu ya ukachenjede ya Mzuzu apsepserezera zionetserozi posindika kuti patsikuli akayenda ku msewu.

Mbusa Levi Nyondo wati PAC ikulankhula zenizeni kotero n’kofunika kuthandizana nayo pa nkhondo yokakamiza boma.

“Mamembala onse ampingo akupemphedwa kuti apite kumsewu kukachita zionetserozo,” adatero Nyondo.

Lamulungu lathali, wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino Saulos Chilima adawerenga kalata ya mpingo ku Parish ya St Patrick mu mzinda wa Lilongwe yomwe imapempha Amalawi kutengapo gawo pa ziwonetserozo.

Share This Post