Chichewa

Kulingalira malumbiro

Listen to this article

Abale anzanga, tidakhala pa Wenela kuonera kulumbiritsa kwa atsogoleri.

Woyamba kulumbiritsidwa adali Adama Barrow wa ku Gambia. Musandifunse kuti ameneyu ndidamudziwa bwanji, chifukwa sindikuyankhani. Mumafuna mumudziwe nokha?

Mwinatu sindidanene. Gambia ndi dziko limene anthu ake adachokera ku Zambia, muja anthu a ku Malawi adachokera ku Malaysia ndipo a ku Austria adachokera ku Australia! Ndife amodzi.

Tsonotu Barrow adalumbilitsidwa kuofesi ya kazembe wa Gambia ku Senegal patatha sabata zingapo atakwapula mkulu uja Yahaya Jammeh pachisankho. Bolatu kwa anzathu amakhala sabata zingapo wina asanalumbire koma pano pa Wenela usiku siudutsa! Mwaiwala kale muja Moya Pete adalumbirira?

Uyu Barrow adalumbira ku Senegal paja chifukwa Yahaya amakana kuchoka pampando. Demokalase ndiye imeneyo! Yaponda yamwa! Yalakwa yalakwa! Yahaya adaziona.

Tsono sindikamba za kulumbira m’dziko la eni. Kodi pa Wenela wina atakana kuti sanapambane pachisankho, wosankhidwa angakalumbire ku Mpanyira patsidya pa Tsangano? Zingatheke wosankhidwa pa Wenela kukalumbira ku Mbeya kapena Masvingo chifukwa sizingatheke pabwalo la pa Wenela?

Winatu amalumbira adali mkulu uja Donal J Trump. Pajatu K2 000 ikutchedwa Trump chifukwa cha kukula mtima kwake. Iyetu adalumbira atagwira mabaibulo awiri. Loyamba lidali la mkulu wamtali uja, Abraham Lincoln. Kukadakhala kuno, bwenzi tikuti Moya Pete adalumbira atagwira baibulo lija adalumbirira gogo uja adandipeza ndikulima kwathu kwa Kanduku.

Koma zingatheke? Ndipo popita kokalumbira, Trump adayamba wamwa tiyi ndi uyu akutulukayu, Barrack Obama. Kenako, onse adakwera galimoto imodzi. Kuno kwathu zingatheke? Abiti Patuma ndi Moya Pete kukwera galomoto limodzi?

Tsonotu sindili pano kukamba za Barrow kapena Trump. Yanga nkhani ndi ya Saulo Chagalauza. Pajatu mkuluyo adabwera ndi moto, kukamba zosintha zinthu kuphiri.

“Mkuluyu lero wangoti ziiii! Sakukambapo kanthu za Joloji Mmera Chadyaka mkulu amene wafufuta chimanga chopezeka pambendera ya Dizilo Petulo Palibe,” adatero Abiti Patuma.

Palibe chimene ndidatolapo.

“Komatu Chadyaka adya ndalama zambiri. Nanga umboni wakuti adanyambita khusa uli kuti?” adafunsa Gervazzio, akuika nyimbo ya Lucius Banda: Mabala.

Malume ndalama kubisa kubanki

Pamene Mbumba yawo ikufa ndi njala

“Adya ndalama bwanji? Zonsetu tiziona mwezi uno ukamatha chifukwa ndiye tsikulo kuli kokakatula ndi sizala,” adatero Abiti Patuma.

Adandipindanso.

“Chomwe ndikunena, uyu Saulo akupenya, akumva ndipo pakamwa ali napo koma sakulankhula. Watsamwa. Mwinatu akuopa Chadyaka paja mpandowu ngolimbirana. Ndani safuna kukhala Barrow kapena Trump? 2019 ndi chaka chinacho,” adatero Abiti Patuma.

Koma uyu bwanji? Adandipindanso!

Gwira bango upita ndi madzi! n

Related Articles

Back to top button