Nkhani

Kumisasa kwabuka matenda a maso, mphere

Listen to this article

Nyumba zawo zudagwa, minda idakokoloka ndipo katundu wambiri kuphatikizapo ziweto zidanka ndi madzi osefukira. Anthu miyandamiyanda, maka akuchigwa cha Shire, adathawira kumtunda kuti apulumutse miyoyo yawo, koma komwe adathawirako nakonso kwaopsa–kwagwa mliri wa matenda amaso ndi mphere m’misasa ya ku Nsanje ndi Chikwawa.

Mneneri wa unduna wa zaumoyo Henry Chimbali watsimikiza izi, koma wati unduna wake ukufufuzabe za anthu amene akhudzidwa ndi matendawa.

mpheleMsasa wa Bitirinyu kwa T/A Nyachikadza m’boma la Nsanje ndiwo wakhudzidwa kwambiri ndi matenda a mphere pamene misasa ya Bereu ndi Kalima kwa T/A Maseya m’boma la Chikwawa ndiwo watekeseka ndi matenda a maso. Msasa wa Bitirinyu ukusunga anthu pafupifupi 6 000.

Pamene Tamvani idazungulira pamsasa wa Bereu ambiri adali koyenda koma mayi Elube Jeke wa m’mudzi mwa Chikutireni adali pamalopo akutonthoza ana ake.

“Mwana wamng’onoyu wayamba kumene [kudwala maso] pamene wamkuluyu ndiye adayamba masiku atatu apitawo. Sakupeza bwino, maso atupa komanso akumadandaula kuti akumva kuwawa.

“Akapeza mtendere ndiye kuti wagona. Sitinalandirepo thandizo chiyambireni matendawa, zomwe zachititsa kuti pakhale kupatsirana,” adatero Jeke uku akufunditsa mwana wokulirapoyo amene ati sakupita kusukulu chifukwa cha mavutowo.

Mavuto sakukata kwa Jeke chifukwa pamene amabwera pamsasawo nkuti nyumba yake itagwa ndi madzi a mvula ndipo katundu wake limodzi ndi munda zidakokoloka.

Poti athawitse moyo, lero wakumana nazonso pamene matenda agwera ana ake. “Sindingakhalenso ndi lingaliro lobwerera kumudzi chifukwa kumenekonso ndiye sikuli bwino. Madzi sadaphwere,” adatero Jeke, kusowa mtengo wogwira.

Mkulu woyang’anira za umoyo pa msasawu, Rodrick Rivekwa, akutsimikiza za matendawa ndipo wati pofika Lachisanu pa 13 March nkuti anthu 15 atapezeka ndi matendawa.

Iye adatinso anthu 10 ndiwo apezeka ndi mphere pamsasawo.

Koma boma lachitapo machawi pofuna kuthana ndi vutoli. “Adatitumizira mankhwala moti anthu onse amene akudwala maso ndi mphere alandira thandizo lachipatala,” adatero Rivekwa.

Iye adati kuchulukana kwa anthu pamsasa wa Bereu lingakhale vuto lina lomwe ladzeetsa mavutowo.

“Tili ndi anthu 1 024, koma malo ogona adali ochepa. Komanso kupeza madzi ndi aukhondo lidali vuto lina. Panopa bolako chifukwa atipatsa zipangizo zosungiramo madzi komanso matenti adationjezera,” adatero Rivekwa.

Nakonso kumsasa wa Kalima mavuto a matenda amaso sadasiye, malinga ndi John Yobe wa m’mudzi mwa Kalima kwa T/A Maseya m’bomalo.

Yobe adathawa m’mudzi mwake ndi kukakhala nawo kumsasawo. Iye akuti adali ndi ziweto monga nkhuku, mbuzi ndi nkhumba zomwe zidatengedwa ndi madzi.

Pokakhala pamsasawu akuti amati ndi chisomo ndipo ankaganiza kuti wapulumuka, koma mwadzidzidzi adadabwa kuona ana ake asanu ndi mmodzi atagwidwa ndi nthenda ya maso.

Yobe akuti pano zinthu zasinthako chifukwa thandizo la chipatala lidafika mofulumira ndipo nthendayi ati sidafale kwambiri monga amaopera.

Malinga ndi nyakwawa Katandika, matendawa adza chifukwa chothithikana pamsasawu, zomwe anthuwa akhala akudandaula.

Koma Chimbali adati unduna wake wafika kale m’malowa kukapereka thandizo la chipatala ndipo zinthu zikusintha.

“Talandiradi malipoti okhudza matenda a maso. Ambiri amene akhudzidwa ndi matendawa ndi ana. Msasa wa Bitirinyu kwa T/A Nyachikadza ndiko talandira malipotiwa. Koma zinthu zasintha chifukwa thandizo lapitako,” adatero Chimbali.

Iye adatinso mavutowa amveka m’maboma a Chikwawa ndi Nsanje kokha pamene m’maboma ena monga Thyolo ndi Mulanje komanso ku Balaka kulibe nkhaniyo.

Mneneriyo adatinso matenda otsekula m’mimba abukanso m’misasayi koma unduna wawo wapereka kale thandizo.

Related Articles

Back to top button
Translate »