Kusanthula khansa ya m’mawere

Petani Mtonga, wachiwiri kwa mkulu wa nthambi ya matenda a khansa kuchipatala cha Queen Elizabeth mumzinda wa Blantyre wati matenda akhansa akagwira mawere amatchedwa khansa ya m’mawere.

Sabata yatha, Mtonga adati matenda a khansa alipo a mitundu ingapo.

Malinga ndi dotoloyu, khansa ya m’mawere imagwira amayi omwe afika msinkhu wobereka ndipo imatha kufalikira kuziwalo zina ngati matendawa  azindikiridwa mochedwa.

Amayi ayenera kudziyesa kaye okha matendawa

“Sabata yatha ndidafotokoza bwino lomwe kuti kwambiri matenda a khansa amayamba okha kotero sizitengera kuti ndi chiwalo chanji chomwe chakhudzidwa ndi matendawa choncho mai aliyense amakhala pachiopsezo cha khansa ya m’mawere. Ngakhale izi zili chomwechi, amayi osuta fodya komanso oledzera amakhala pachiopsezo chachikulu chifukwa mufodya ndi mowa m’mapezeka zinthu zomwe zimakolezera matendawa,” iye adatero.

Dotoloyu adati zizindikiro za khansa ya m’mawere ndi monga kutuluka zotupa m’mawere, kuchita zilonda m’mawere, kutulutsa magazi m’mawere ndi kusintha mtundu kwa mawere.

Iye adati mayi wina aliyense, makamaka yemwe wafika msinkhu wobereka amayenera kumadziyeza yekha pamene akusamba kapena akamaliza kuti ngati angaone zinthu zodabwitsa, athamangire kuchipatala ndipo pakutero, imazindikiridwa mwachangu.

“Amayenera kumadziyang’anira pagalasi makamaka lalikulu lapakhoma kuti athe kumadziona bwinobwino ataimirira ndipo akaona kuti bere kapena mawere asintha mtundu kapena akuoneka kukula kusiyana ndi poyamba, athamangire kuchipatala.

“Njira ina, mayi amatha kuimirira kapena kugona pansi ndi kuyamba kusindikiza bere lakumanzere ndi chikhatho chamkono wakumanja mozungulira, ndi kubwerezanso ndi bere lakumanja momvetserera bwino ndipo akaona kuti mukumveka kanthu kalikonse kachilendo, athamangire ku chipatala,” iye adatero.

Mtonga adaonjeza kuti pali zikhulupiriro zosiyanasiyana zomwe zimatha kuyambitsa khansa  m’mawere zomwe zilibe umboni ndipo mu mndandanda wa zomwe zimayambitsa matendawa ku ziwalozi mulibe. Iye adati zinthuzi ndi monga kuika foni za m’manja m’mawere, kuvala khamisolo wa pa kaunjika ndi zina zambiri. n

Share This Post

One Comment - Write a Comment

Comments are closed.