Nkhani

Kusefukila kwa madzi: Amtauni  aiwalidwa?

Listen to this article

Maso a mabungwe komanso boma ndi anthu onse ali kuchigwa cha mtsinje wa Shire komwe anthu ambiri adakhudzidwa ndi madzi osefukira.

Aliyense amene wapeza thandizo, akumatsetserekera kumabomawa poiwala kuti madera enanso ali pamoto ndikugwetsedwa kwa nyumba zawo.

Floods have destroyed houses in the affected districts

Mwachitsanzo, mumzinda wa Blantyre, anthu ambiri adakhudzidwa ndi ngoziyi koma thandizo lakhala likungopita ku Chilobwe, Chimwankhunda ndi maboma ena monga Mulanje, Thyolo ndi ena akuchigwa cha mtsinje Shire.

Sabata yathayi, bungwe la Self-Help Assistance Program (Asap) mogwirizana ndi IM Swedish Development Partner lidazungulira mzinda wa Blantyre, ukotu ndi kwa T/A Makata komwe adagwidwa tsemwe kuona momwe anthu akuvutikira chifukwa cha ngozi ya madzi.

Anthutu akusowa pokhala ndipo ana ang’onoang’ono monga ali pachithunziwa agwidwa njakata chifukwa cha mvula yosaleka yomwe idagwa pa January 11.

Bungweli lidaperekako matani 25 000 a ufa wachimanga, matani 2 500 a nyemba kwa mabanja 540 amene adakhudzidwa ndi ngoziyi.

Banja lililonse lidalandira thumba lolemera makilogalamu 50 a ufa ndi makilogalamu 5 a nyemba. Katunduyu adali wokwana K6.7 miliyoni.

Mkulu wa bungweli Twisiwile Mwaighogha, adati nawonso adali wodzidzimuka kuti anthu ambiri akuvutika motere koma dziko silikudziwa.

 

 

Related Articles

Back to top button
Translate »