‘Kusintha lamulo la ufiti kwachedwa udyo’

Kuchedwa kwa ntchito yosintha lamulo lokhudza zaufiti kukuchititsa kuti okalamba amene akuwaganizira kuti ndi mfiti apitirire kuzunzidwa komanso kuphedwa, atero a mabungwe ena.

Polankhula ndi Msangulutso padera-padera, mkulu wa bungwe limene limati kulibe ufiti la Association for Secular Humanism (ASH) George Thindwa komanso mkulu wa bungwe losamalira achikulire la Friends of the Elderly Mike Magelegele ati kuchedwa kwa ntchitoyi kukuchititsa kuti nkhanza kwa okaikiridwa ufiti zipitirire.

Akuchulukira ena akuzuzidwa mpaka kuphedwa chifukwa chowakaikira ufiti

Nthambi yapadera younikira zosintha malamulo okhudza zaufiti ya Special Commission on Review of the Witchcraft Act yakhala ikumva maganizo a anthu pa zosintha malamulowo ndipo ikuyembekezeka kumaliza zonse mu July chaka chino. Ntchito yofufuzayi idayamba zaka 10 zapitazo.

Thindwa adati: “Ntchitoyi ikuchedwa chifukwa cha ndondomeko yomwe bungwe lofufuzalo likutenga komanso akusowa thandizo. Mmalo molunjika pa zaufiti kuti athetse vuto, iwo afika mpaka kukambirana za chipembedzo cha satana.”

Iye adati izi zili apo, nkhalamba zina zikuvutitsidwa komanso kuphedwa pachabe chifukwa palibe umboni wa ufiti.

Malinga ndi Thindwa, lamulo latsopano la ufiti likuyenera kulunjika poti aliyense wonena mnzake kuti mfiti aziyankha mlandu wothera kundende osapatsidwanso mpata wopereka chindapusa.

“Ena amangowanamizira agogo kuti ndi mfiti kuti awalande minda,” adatero Thindwa.

Magelegele adati bungwe lake lakhudzidwa chifukwa cha kuchedwa kwa ntchitoyi chifukwa ambiri ataya miyoyo yawo.

“Tikupempha boma  kuti tigwirane manja poyesetsa kuti zinthu zisinthe,” adatero Magelegele.

Iye adatinso chiyambireni chaka chino paphedwa agogo 8, zomwe zikungoonetsa kuti ntchito ndiyaikulu.

Dziko lino likugwiritsa ntchito lamulo la chitsamunda lomwe lidakhazikitsidwa mu 1911 loti kulibe ufiti. Koma pomwe ntchitoyi ikuyenda pang’onopang’ono  ngati nkhono, agogo akupitirira kuvutika.

Komatu akadaulo pa malamulo, kaganizidwe komanso mafumu akukhulupilira kuti mchitidwewu ukhonza kuchepa ngati lamuloli lingakhazikitsidwe mwa changu.

Mmodzi mwa katswiri pa kaganizidwe pachipatala cha amisala cha  St John of God ku Mzuzu, Ndumanene Sulungwe adati agogo ambiri amaphedwa

chifukwa chodwala nthenda yoiwala, zimene zimachititsa kuti akamafunsidwa mafunso pamene akukaikiridwa ufiti amayankha zosemphana.

Iye adati ena mwa agogowa amaiwala ngakhale dzina la mudzi wawo kumene ndipo anthu akawapeza ali obalalika chomwecho, amati ndi mfiti ndi kuwachita chipongwe.

Choncho iye adapempha omwe akukonza lamulolo kuti ayesetse kuteteza agogowa.

Polankhulapo wachiwiri kwa mkulu  woyendetsa ntchitoyi, Clotilda Sawasawa adavomereza kuti agogo, alubino ndi ana ndi amene ali pampani pa nkhani zokhudzana ndi kukayikiridwa ufiti.

Ndipo Sawasawa adavomerezanso kuti ntchitoyi yakhala isakuyenda mwachangu chifukwa chosowa ndalama.

“Ndalama zoyendetsera ntchitoyi zakahala zikutivuta, choncho sizimayenda kwenikweni koma pano tiyesetsa kuthamangitsa zinthu kuti pofika mwezi wa July chaka chino tikhale titamaliza kutolera maganizo,” adalongosola motero.

Ngati mmodzi mwa anthu okhudzidwa ndi nkhanizi, Chistopher Ndovi yemwe ndi wa chi alubino adauza Msangulutso kuti wakhala akuvutitsa kuchokera ali wachichepere.

“Padali nthawi ina, mnzanga ankafuna nyama yochokera kumbuyo kwa khosi langali ndi tsitsi langa la pankhongo kuti akapangire mankhwala.

Zidafika povuta mpaka kumanditsatira kunyumba. Koma agogo anga ndiwo adanditeteza,” adalongosola Ndovi.

Nayo Mfumu Mwenemsuku yochokera m’boma la Chitipa idati ndi zoona kuti agogo ndi ana ndiwo akukhudzika kwambiri ndi zaufiti.

Iye adati ana ambiri akumaulula kuti agogo ndiwo akuwaphunzitsa ufiti ndipo pena agogowa amalephera kudzifotokoza pomwe nthawi zina amavomera ndithu.

Share This Post