Nkhani

Kusowa kwa shuga kudzetsa kulira kwa Amalawi

Listen to this article

Amalawi m’dziko muno ati sakudziwa chomwe chikuchitika m’dziko muno kotero boma likuyenera kubweretsa mayankho mwachangu zinthu zisadavute.

Izi zadza pomwe m’mizinda ikuluikulu yadziko lino ya Blantyre, Lilongwe ndi Mzuzu mudali mizere ya anthu ofuna shuga.

Ndemangazi zadza m’sabatayi pomwe mavuto a kusowa kwa shuga adayala paliponse m’dziko muno.

Anthuwa ati boma likuyenera kuganizira moto wa anthu chifukwa ndiwo adasankha bomali kuti lidzitandiza zomwe akukumana nazo.

Ruth Samikwa wa ku Ndirande mumzinda wa Blantyre wati kumeneko pofika Lachitatu amagula sugar woyera pa mtengo wa K400.

“Zinthu zavuta ndipo sindikudziwa ngati sitithawa m’dziko muno. Shuga wa bulawuni adasowa kalekale pano yemwe akupezeka mwa apo ndi apo akupanga K400,” adatero Samikwa.

Thocco Loga wa ku Kawale mumzinda wa Lilongwe wati kumeneko ndiye zafika ngati akusaka mafuta agalimoto.

“Moyo wasinthiratu moti chifukwa tiyi ndidamwa kale. Shuga akupezeka koma uyambe wavutika ngati ukufuna umupeze ndipo akugulitsidwa pa K450,” adatero Loga.

Mwezi wangothawu shuga wa dziko lino wakhala akugwidwa ku Tanzania ndi maiko ena.

Related Articles

Back to top button