Kutambasula mwambo  wa mafumu wa mkangali

April 10, 2015 • Kucheza • Written by :

Mwambo wa mkangali umachitika pakati pa Achewa nthawi yotulutsa anamwali. Kalelo akuti anthu amaloledwa kukatomera mbeta kutsimba kuti akatuluka amukwatira. TAMVANI adacheza ndi Gulupu Chatata ya m’dera la T/A Chitukula ku Lilongwe ndipo machezawo adali motere:

 

Chatata: Kholo limatha kupereka mwana kuti akalangidwe

Chatata: Kholo limatha kupereka mwana kuti akalangidwe

Achewa amakhulupirira kulowetsa ana gulewamkulu. Kodi zimenezi zimachitika nyengo iti?

Gulewamkulu timalowetsa ikatha nyengo yokolola chifukwa nyengoyi ntchito zambiri zimakhala zitatha ndiye mpomwe pamachitika miyambo yambiri monga

ziliza, zizangala ndi mkangali ndiye timatengerapo mwayi kuchita miyambo ngati imeneyi.

 

Mkangali nchiyani?

Mkangali ndi mwambo wa mafumu pomwe amapereka mwambo kwa anamwali. Chomwe chinkachitika kalelo nchakuti anamwali akakhala pafupi kutuluka akatha

kulandira mwambo, amuna amaloledwa kupita kukapereka ndalama kwa mafumu aja ndi kutomera kuti namwali yemwe akufunayo akatuluka adzakhale wawo ndiye

amangoti mwambo wa mafumu. Mafumuwo ndiwo amakayendetsa zonse kwa makolo a namwaliyo kuti banja litheke.

 

Masiku ano zimenezi zimachitikabe?

Ayi, masiku ano zidatha malingana ndi matenda adabwerawa chifukwa mwamuna aliyense ngakhale wokwatira kale bola ngati ali ndi ndalama amatha kukatomera koma pano sizingatheke.

 

Kutsimbako kumakhala zotani?

Kutsimba nchimodzimodzi kudambwe kumakhala anamwali ndi aphungu awo omwe amayendetsa ntchito yonse yopereka mwambo. Nkhani yaikulu imakhala kupereka

mwambo wa mmene munthu amayenerera kukhalira m’mudzi komanso m’nyumba mwa makolo ake. Pena amathanso kulangidwa za thupi la munthu kuti azikhala

odzilemekeza, asamangoti yambakatayambakata.

 

Nkhaniyi inayamba ndi kudambwe. Talongosolani, kodi onka kudambwe amayenera kukhala otani?

Kalelo timasankha achinyamata a zaka kuyambira 10 omwe amaoneka kuti ayamba kuchangamuka koma pano nkutsukuluzika kwa miyamboku angopita aliyense.

Nthawi zina kholo limatha kupereka mwana wake kuti akalangidwe makamaka akakhala ndi khalidwe loipa, lamwano.

 

Mwambo umasiyana bwanji pakati pa achinyamata opita okha chifukwa cha msinkhu ndi omwe amatumizidwa ndi makolo chifukwa cha mwano?

Pamakhala kusiyana kwambiri. Mwambo wina wonse amatha kulandirira limodzi koma ochita kutumizidwa kaamba ka mwano amakhaulitsidwa n’kukwapulidwa ndipo

kukuuzani zoona kumakhala kukwapula moti akatuluka zoti ndi kukayambiranso khalidwe loipalo ndiye kuti adalidi nkhutukumve mwanayo.

 

Nanga kwa omwe samafuna kulowa gulewamkulu zimakhala bwa?

Pamwambo wa Achewa, munthu aliyense, makamaka mwamuna, amayenera kulowa gulewamkulu chifukwa pamudzi pamakhala zinthu zambiri zoyenera kuchitira limodzi ndiye wosalowa amatengedwa ngati mwana choncho samaloledwa kutenga nawo mbali. Pachifukwachi, munthu aliyense amayenera kulowa, ngakhale omwe ali azibusa panowa ambiri adalowapo gule n’kuchita kusiya.

 

Pokalowapo, munthu amayenera kutenga chiyani?

Pokalowa munthu amayenera kutenga mpeni wokachekera nyama kudambweko komanso chofunda chifukwa akatero amakhala kuti watuluka m’nyumba ya makolo ndipo

tsopano azikagona ndi anzake kumphala.

 

Ena amanena kuti uyenera kubweretsa nkhuku, njachiyani?

Nkhuku imakhala kumapeto mwambo wonse ukaperekedwa. Phungu akakhutira kuti namwali wake wapsa, amakatenga nkhuku yopangira mphundabwi kuti namwaliyo

akadya asamaiwale mwambo.

 

Amayi aja amakhala ndi gulewamkulu amakhalanso olowa?

Bwinobwino. Kugulewamkulu kuli gule yemwe mumafunsa uja wa chisamba, ndiye amayi ambiri amalowa chisambacho koma ofuna amatha kulowa ndithu kudambwe

mpaka kumawedza gule. Abambonso akafuna amatha kulowa chisamba bwinobwino chifukwa ndi mwambo.

 

All views expressed in the comments of users of www.mwnation.com are independent. They are not a reflection of the views of Nation Publications Limited (NPL) nor are they endorsed by NPL. This is a forum provided by NPL to make good on it's corporate slogan of Making freedom of expression a reality.

Comments are closed.

« »