Nkhani

Kuthimathima kwa magetsi kwakhudzanso akumidzi

Listen to this article

Ndi Lolemba mmbandakucha wa pa 12 September, nthawi yangokwana kumene 4 koloko koma magetsi azima kale m’boma la Mulanje. Chiyembekezo nchoti posakhalitsa ayaka.

Gulu la alimi lopanga tsabola wa Zikometso Hot Chilli Sauce, maso akudikira kuti mwina magetsi ayaka nthawi iliyonse. Poyembekezera, asakaniza kale tsabola kuti magetsi akangoyaka ayambe kuphika m’makina awo.black-out

Akadadziwa akadaphika therere! Magetsi sadayake tsiku lonse. Pofika 7 koloko mmawa wa Lachiwiri, magetsi kuli chuu, zomwe zapangitsa kuti akataye zosakanizazo.

Umu ndi momwe zikukhalia kwa anthu akumudzi amene sangakwanitse kupeza injini ya magetsi (generator).

Makampani a alimi akulephera kuyendetsa malonda awo, zinthu zasokonekera chifukwa cha kuthimathima kwa magetsi, komwe kukulowa mwezi wachiwiri tsopano m’dziko muno.

Nalo bungwe lopanga ndi kugulitsa magetsi la Escom laneneratu kuti mavutowa anyanyira miyezi ikubwerayi chifukwa cha kuchepa kwa madzi omwe amapukusa makina opangira magetsi ku Nkula ndi ku Tedzani  mumtsinje wa Shire.

Monga akufotokozera wachiwiri kwa mkulu wa Zikometso, Amos Ambali, pasabata amapanga mabotolo a tsabola 2 100, koma pano akupanga osaposera 500.

“Timagwira ntchito Lolemba mpaka Lachisanu, koma masiku onsewa kukukhala kopanda magetsi. Mapeto ake tayamba kugwira usiku wokhawokha komanso Loweruka masana pamene magetsi akumayaka.

“Sizikupanganika, pena kukukhala kopanda magetsi tsiku lathunthu, zomwe zasokoneza bizinesi yathu. Kangapo konse tataya tsabola patatha masiku awiri popanda magetsi kupangitsa kuti tsabola wathu aonongeke,” adatero Ambali.

Nawo a Talimbika Agro-Processing and Marketing Cooperative Society, amene amapanga mafuta ophikira a Sunpower m’boma la Salima, akuti magetsi akazima, amagulula makina awo ndi kuchotsa mpendadzuwa yense.

Fanny Jodani ndi mmodzi mwa akuluakulu pa Talimbika ndipo akuti patha miyezi iwiri magetsi akuzimazima ndipo tsiku lililonse akumazima isadakwane 4 koloko n’kumayaka 6 madzulo.

“Apapa tayamba kugwira ntchito usiku, komabe zikuvuta chifukwa pena kukumakhala kopanda magetsi. Magetsi akazima sitigwira ntchito ndipo timagulula makina athu, kuchotsa mpendadzuwawo,” adatero.

Talimbika imapanga malita 500 patsiku ngati magetsi akuyaka, koma pano tsiku likutha osapanga mafuta.

Ali ndi antchito oposa 11 amene akufunika malipiro, kodi akumawalipira bwanji?

Mkulu wa Talimbika, Pharison Chiwoko, akuti ili ndi vuto lalikulu.

“Magetsi akamayaka bwino, timapanga ndalama yoposa K3 miliyoni pamwezi. Mwezi unowo ngakhale K1 miliyoni sikwana. Timaononga K700 000 kuti tilipire antchito. Mutha kuona kuti mwezi uno ngati anthu alandire ndi mwayi,” akutero Chiwoko.

Nako ku Dowa zinthu sizili bwino. Watson Kamchiliko mkulu wa Madisi Agro-Processors Cooperatives, omwenso amapanga mafuta ophikira, wati pali mantha kuti angachotse antchito ena ngati sizisintha.

“Timapanga malita 2 000 patsiku. Lero zasintha, tikumapanga malita 2 000 pasabata, bizinesi yasokonekera. Tili ndi ogwira ntchito amene akulandira K150 000, kodi awa tingawalipirenso?” adatero Kamchiliko.

Nako kuchigayo kwasokonekera. Kamchiliko akuti anthu akugona kuchigayo kudikira kuti magetsi ayake pa boma la Dowa.

“Pena amayaka cha m’ma 10 koloko usiku, anthu amagona kuchigayo kuti akayaka agaitse,” adatero.

Kwa T/A Phambala m’boma la Ntcheu, eni zigayo za dizilo apezerapo mwayi ndi kuzimazima kwa magetsi pamene akweza mtengo kuchoka pa K300 thini kufika pa K350.

Koma uthenga kuchokera kubungwe la Escom sukupereka chiyembekezo kwa anthuwa.

Mkulu wa bungweli, John Kandulu, akuti izi zikhala zikuchitika kuyambira mwezi uno mpaka December pamene mvula idzakhale itayamba.

Kandulu akuti izi zili chonchi chifukwa mlingo wa madzi a mumtsinje wa Shire ndi wotsika ndipo kutsikaku kupitirira pokhapokha mvula itayamba.

“Chifukwa cha izi, tingokwanitsa kutapa 135 megawatts mmalo mwa 361 megawatts zomwe zichititse kuti magetsi akhale akuzimazima,” adatero Kandulu.

Related Articles

Back to top button