Nkhani

Kuyamba kwa zipolowe

Listen to this article

 

Malipoti m’dziko la South Africa akhala akumveka kuti mfumu ya mtundu wa Chizulu Gooodwill Zwelithini ndiyo idakolezera moto pamene idalankhula kuti mzika za m’maiko ena zibwerere kwawo ponena kuti zikuwaphangira ntchito.  Malipotiwo adati pamsonkhano wina ku Polonga m’dzikolo, mfumuyo idati anthu achilendo,a mene amatchedwa makwerekwere ku South Africa apakire tawo nkubwerera kumudzi.SA-violence_xenophobia

Malipotiwa atangomveka, anthu obwera akhala akuona zakuda ndi mzika za m’dzikomo ndipo anthu oposa 7 aphedwa, mwa iwo awiri ndi a m’dziko muno ndi ena kuvulazidwa.

Ngakhale utsi sufuka popanda moto, Lolemba Zwelithini adakana izi pamene amalankhula pabwalo la Moses Mabhida ataitanitsa mafumu, mamulumuzana ndi ena onse m’dzikomo ndipo adati atolankhani ndiwo sadamumvetse zomwe ankanena.

Maiko komanso mabungwe mu Africa akhala akudzudzula zomwe zikuchitika m’dzikolo.

Dziko la Nigeria nalo lidayamba kusala nzika za dziko la South Africa moti pofika Lachitatu, ofesi ya kazembe wa South Africa ku Nigeria adaitseka.. Ku Zimbabwe, wailesi za m’dzikolo zidasiya kuimba nyimbo za m’dziko la South Africa. Pamene ku Mozambique, nzika zina za m’dziko la South Africa zidachitidwa chipongwe ndipo galimoto zina za ku South Africa zidatenthedwa..

Ku Malawi anthu adachita zionetsero Lachiwiri pamene adakapereka chikalata cha madandaulo awo kwa kazembe wa dziko la South Africa.

Lachisanu, amayembekezekanso kuchita zionetsero kukakamiza kuti mashopu a m’dziko la South Africa amene ali m’dziko muno monga Shoprite, Game ndi PEP asagulidwenso. n

Related Articles

Back to top button