Nkhani

Kwadza kaundula wa foni za m’manja

Listen to this article

Eni lamya za m’manja m’dziko muno akuyenera kulowa m’kaundula wa umwini wa lamya zawo kuti azitha kugwiritsa ntchito lamya zawozo, yatero nthambi yoyendetsa ntchito za mauthenga ya Malawi Communications Regulatory Authority (Macra).

Ngakhale anthu ena akusonyeza kusagwirizana ndi mfundoyi, mkulu wa bungwe loyimirira anthu ogwiritsa ntchito zinthu la Consumers Association of Malawi (Cama) John Kapito wati kaundulayu ngofunika.

M’chikalata chake, Macra yati munthu aliyense yemwe ali ndi lamya ya m’manja ndipo sadalowe mkaundulayu pofika pa 31 March 2018, nambala yake idzasiya kugwira ntchito.

“Lamulo la mauthenga limene lidakonzedwa mu 2016 limapereka mphamvu ku Macra yokakamiza munthu aliyense yemwe ali ndi lamya ya m’manja kulowa m’kaundula wosonyeza umwini wa nambala ya lamya yakeyo,” yatero Macra.

Koma anthu ena ati akudabwa kuti akaundula ayamba kuchuluka m’dziko muno makamaka pano pomwe tikuthamangira 2019 chaka cha chisankho cha pulezidenti, aphungu ndi makhansala.

“Akaundula amenewa adali kuti nthawi yonseyi ndipo cholinga chake n’chiyani? Bwanji akuoneka ngati akuchitika mwaphuma chonchi osayamba atiuza ubwino ndi kufunika kwake,” adatero Andrew Chisomo Mwale wa ku Ntchisi.

Maganizo akewa adafanana ndi maganizo a anthu ena omwe Tamvani adacheza nawo pa nkhaniyi m’maboma a Lilongwe ndi Dowa.

Pothirirapo ndemanga, Kapito adati dziko la Malawi limatsalira pankhaniyi chifukwa maiko ena adayamba kale kuchita kalembera wa mtunduwu.

“Ili ndi lamulo ndipo dziko la Malawi limatsalira. Mmaiko ena sungangogula khadi la lamya pamsewu n’kuyamba kugwiritsa ntchito osalowa m’kaundula n’chifukwa chake anthu amangogula khadi n’kupangira zolakwika n’kuyitaya,” adatero Kapito.

Iye adati anthu akakhala m’kaundula wa lamya, munthu amakhala ndi mwayi wofufuza yemwe wamulankhulira zoipa, zoopseza kapena kumuchita chipongwe pa lamya ndipo zimachepetsa mchitidwe ochita upandu mozemba.

Macra yati eni lamya la mmanja akuyenera kupita ku ofesi ya netiweki (Airtel, Tnm, Access ndi MTL) ndi chitupa monga pasipoti, Drivers Licence, chitupa cha unzika komanso umboni wa makolo kwa ana awo.

Mkaundulamo, muzifunika dzina la mwini nambala, ngati ali wa mwamuna kapena wa mkazi, tsiku lobadwa, nambala ya chizindikiro ndi keyala ya munthuyo kapena satifiketi ya bizinesi ngakhalenso yolipirira msonkho kwa omwe ali ndi lamya ya bizinesi.

Chifukwa chopanda kaundulayu, anthu ena akhala akupanga upandu pogwiritsa ntchito lamya za mmanja monga kutumizira mauthenga abodza ndi cholinga chobera azawo, kuopseza anzawo ndi kuipitsa mbiri za anthu ena pozindikira kuti sadziwika.

Related Articles

Back to top button
Translate »