Chichewa

La Nina wachita katondo

Mmene mitambo ya mvula imachita mikhwithi ndipo mvula idayamba kugunda, gogo Justina Nya Chilembo, wa zaka 65, adali ndi chisangalalo komanso chiyembekezo kuti chaka chino abzala msanga.

Gogoyu, wa m’mudzi mwa Chibo, kwa Paramount Chief Chikulamayembe m’boma la Rumphi, sadayembekezere kuti akhala mmodzi mwa anthu oyambirira kumva ululu wa nyengo ya La Nina, imene mvula imagwa mosakaza.

Nyumba yake ya zipinda zitatu momwe amakhala ndi ana aamuna awiri kuphatikizapo wamkazi ndi zidzukulu zingapo, idasasuka denga lofolera ndi malata, kaamba ka chimvula chomwe chidabwera ndi chimphepo chamkuntho sabata ziwiri zapitazo m’deralo.

Chifukwa sadakonzekere za ngozi yotere, gogo Nya Chilembo, yemwe ndi wamasiye, pano akusowa mtengo wogwira chifukwa katundu wambiri m’nyumbamo, kuphatikizapo chakudya, adaonongeka.

“Sindikudziwa kuti nditani nawo anawa ndi zidzukuluzi tsopano…Sindikudziwa komwe ndingapeze ndalama zoti n’kufoleranso nyumbayi, kaya nditani ine wamasiye!” adalira choncho, poyankhula ndi Tamvani m’sabatayi.

Nya Chilembo: Sindikudziwa nditani

Anthu ambiri m’derali ndi madera ena m’dziko muno adakhudzidwa chimodzimodzi ndipo akusowa mtengo wogwira chifukwa mvulayo idawadzidzimutsa ndi magwedwe ake osakaza.

Inde, yafikanso nyengo yolira pamene madzi osefukira ndi mvula yodza ndi mphepo yamkuntho zasamutsa kale anthu komanso kugwetsa nyumba m’maboma 13 m’dziko muno.

Naye Chimwemwe Bonifasiyo wa m’mudzi mwa Chikaola kwa T/A Kachindamoto ku Dedza adati nyumba yake idasasuka ndi mvula ya mkuntho yomwe idagwa kumeneko.

“Ndidathawa pakhomo ndipo ndidabwera mvula itatha. Katundu adanyowa komanso nyumba idasasuka,” adatero.

Ndipo Felina Kuyaka wa m’mudzi mwa Pemba kwa Senior Chief Kawinga m’boma la Machinga wati pano akugona m’kitchini kutsatira kugwa kwa nyumba yake.

Kuyaka akuti ana ake atatu adavulala ndi mvulayo.

“Nyumba idagwa, ana avulala ndipo ali kuchipatala. Katundu adaonongeka,” adatero Kuyaka.

Mneneri wa nthambi ya boma yoona ngozi zogwa mwadzidzidzi ya Department of Disaster Management Affairs (Dodma), Jeremiah Mphande watsimikiza kuti padakalipano, vutoli lakhudza maboma a Balaka, Machinga, Mangochi, Nsanje, Dedza, Dowa, Karonga, Rumphi Mzuzu, Chiradzulu, Phalombe, Zomba ndi Nkhotakota.

Iye adachenjeza anthu amene akukhala malo angozi monga odikha kuti asamuke, ndipo adaonjeza kuti nthambiyo yakonzeka kuthana ndi mavutowa.

“Tidadziwitsidwa mmbuyomu ndi anzathu amene amalosera momwe nyengo ikhalire amene adatiuza kuti tikhala ndi mvula yambiri chifukwa cha nyengo ya La Nina.

“Pachifukwachi, tidafika m’maboma onse ndipo tidaikamo gulu lomwe lizitipatsa malipoti zikangochitika komanso thandizo lomwe likufunika,” adatero Mphande.

Ngakhale nthambiyo yakonzeka, Mphande adati kupewa kuposa kuchiza kotero anthu amene akukhala malo angozi asamukiretu zinthu zisadafike poipa kwambiri.

“Okhala madera amene madzi atha kufika, ayenera kusamukira kumtunda chifukwa chaka chino tilandira mvula yambiri. Iyi ndi njira yokhayo yopewera mavutowa,” adatero Mphande.

Iye adati chaka chino chingathe kuposa chaka chatha chifukwa mvula yangogwa sabata zochepa koma madera amene samachitikachitika ngozi akhudzidwa.

“Ndi chisonyezo kuti zinthu ziipa chaka chino. N’chifukwa tikuti anthuwa asamukire kumtunda,” adaonjeza.

Nthambi yoona za kusintha kwa nyengo ya Department of Climate Change Management and Meteorological Services idalosera kuti chaka chino kukhala nyengo ya La Nina yomwe ingapangitse kuti kukhale napolo.

Malinga ndi nthambiyo, La Nina amapangitsa kuti mvula ibwere yochuluka ndipo zigawo zakummwera ndi kumpoto kwa dziko lino ndi komwe adati kugwa mvula yoposera mlingo wake. Zamveka kuti munthu mmodzi wafa pangozi ya mvula.

M’boma la Balaka, mvula ya mkuntho yasokoneza midzi ya mwa T/A Chanthunya ndipo nyumba 278 zasasuka. Sukulu komanso nyumba zopemphereramo zagwa ndipo anthu anayi avulala.

Malinga ndi lipoti la ofesi ya DC, mvula ya mkuntho ndiyomwe idavuta kumeneko ndipo anthu akusowa pokhala komanso minda yawo yakokoloka.

Ku Karonga, mvula ya idasakaza ndi kugwetsa nyumba 106 kuyambira pa November 30 mpaka December 2 m’madera a T/A Wasambo ndi Senior Chief Kyungu.

Lipoti la DC lati anthuwa akusowa pokhala komanso akusowa chakudya ndipo akufunika thandizo lachangu.

Ku Machinga nyumba 395 zasasuka komanso nyumba zopempherera ndi sukulu zasasuka.

Wothandizira mkulu woona za ngozi zogwa mwa dzidzidzi m’bomalo, Shephard Jere, adati nyumbazi ndi za mwa T/A Chikweo, Kawinga ndi Nkoola.

Ku Mangochi, ngozi ya mvula yamphepo idachitika pa 5 December ndipo nyumba 587 zidagwa malinga ndi lipoti la wothandizira mkulu woyang’anira ngozi zogwa mwadzidzidzi Carlo Chabwera Millinyu.

Ku Dedza, nyumba 196 zagwa chifukwa cha mvula ya mphepo ndipo mayi mmodzi adamwalira komanso ena kuvulala. Izi zidachitika m’dera la T/A Kachindamoto komanso Chilikumwendo.

Malinga ndi lipoti la DC wa bomalo James Kanyangalazi, mabanja okhudzidwawa akufunika thandizo lachangu zomwe ndi malo okhala komanso chakudya.

Ku Dowa, nambala ya mabanja amene akhudzidwa sadadziwike koma ma T/A atatu ndiwo akhudzidwa monga Chakhaza, Chiwere ndi Msakambewa.

Maboma ena amene akumana ndi ngoziyi koma malipoti sadalembedwe ndi Mzuzu, Chiradzulu, Nkhotakota, Nsanje, Zomba ndi Phalombe. n

Related Articles

Back to top button