Nkhani

Lamulo lochotsa mimba ladengula

Listen to this article

… Akufuna ogwiriridwa, opatsana pathupi pachibale ndi ana achichepere aziloledwa kuchotsa pathupi

 

Lamulo lokhudza kuvomereza kuti amayi akhoza kumachotsa mimba movomerezeka latsala pang’ono kupita ku Nyumba ya Malamulo kuti aphungu akalikambirane, Msangulutso watsinidwa khutu.teen-pregnancy

Mlangizi wa mmene ntchitoyi ikuyenera kuyendera kubungwe lomwe likulimbikitsa kuti boma livomereze kuchotsa mimba popanda mlandu la Coalition on Prevention of Unsafe Abortions (Copua), Luke Tembo, wati kukonza lamuloli kudatha kale ndipo kwatsala kuti aphungu akalikambirane.

“Tidasiya nkhaniyi m’manja mwa nthambi ya zamalamulo (Law Commission) kuti aunike lamulo lomwe lidalipo kale ndipo tikunena pano lamulo lina lidatha kale kukonzedwa ndipo likungodikira kupita ku Nyumba ya Malamulo,” adatero Tembo.

Wothandizira ntchito zounika malamulo kuthambi ya zamalamulo, Mtamandeni Liabunya, Lachisanu adatsimikiza kuti nthambiyi idamalizadi kukonza lamulo latsopanoli ndipo kwatsala kuti liyende mundondomeko zina lisadasindikizidwe.

“Zonse zoyenerera zidachitika kale ndipo tidamaliza, pano tikungoyembekezera kuti tikatule kuunduna woona kuti pasamakhale kusiyana pakati pa amuna ndi akazi komanso chisamaliro cha ana kuti ndondomeko izipitirira mpaka ku Nyumba ya Malamulo,” adatero Liabunya.

Nduna yoona kuti pasamakhalae kusiyana pakati pa amuna ndi amayi komanso chisamaliro cha ana, Patricia Kaliati, adati unduna wake sukudziwapo kanthu pa za lamulo latsopanoli.

Kaliati: Sitingalole zimenezo
Kaliati: Sitingalole zimenezo

Iye adati ali ndi njala yoona lamulolo kuti aone ngati zomwe zilimo zikugwirizana ndi zolinga za boma pa za tsogolo ndi moyo wa amayi ndi asungwana.

“Nkhaniyitu okhudzidwa kwambiri ndi amayi ndi asungwana

ndiye ife ngati unduna wa boma, sitingalole chilichonse chomwe chikusemphana ndi mfundo za boma zotukulira amayi ndi atsikana. Atipatse tilione lamulolo ndipo tiliunike,” adatero Kaliati.

Bungwe la Copua likulimbikitsa zobweretsa lamulo latsopanoli pofuna kuchepetsa imfa za amayi ndi asungwana komanso ana chifukwa cha njira zochotsera mimba zamseri poopa kuti kuchipatala sakaloledwa komanso angaimbidwe mlandu wofuna kupha.

Tembo adati lamulo lakale limangolola munthu kuchotsa pathupi pokhapokha ngati pali umboni wakuti moyo wa mayiyo kapena mwana uli pachiopsezo. Koma lamulo latsopanoli laonjezerapo zifukwa zina zochotsera mimba.

“Lamulo latsopanoli lawonjezera zifukwa zina zomwe munthu angathe kuchotsera mimba, monga mimba yobwera kaamba kogwiriridwa; mimba yopatsana pachibale; mimba zopatsana ana [osakhwima pamchombo]; komanso amisala aziloledwa kuchotsa mimba,” adatero Tembo.

Kaliati adati unduna wake sugwirizana ndi ganizo lovomereza kuchotsa mimba kaamba kakuti uku n’kuphwanya ufulu wa mwana wosabadwayo.

Iye adati akudziwa zoti magulu ena akulimbikitsa zokhazikitsa lamulo lovomereza kuchotsa pakati, koma boma lidanena kale poyera kuti kuteroko n’kusokeretsa mtundu wa Amalawi, makamaka asungwana.

“Kodi kuuza anthu uti akhoza kumachotsa mimba mmene afunira ndiye kuti tikumanga dziko lanji? Zimenezi zikhoza kuchititsa kuti anthu, makamaka asungwana, atayirire podziwa kuti akatenga mimba akachotsa,” adatero Kaliati.

Iye adati boma limangovomereza lamulo lomwe lilipo pakalipano lomwe lidayamba kuonetsa mphamvu m’chaka cha 2010. Lamuloli limalola munthu yemwe moyo wake uli pachiwopsezo kuchotsa pathupi.

Wapampando wa komiti ya aphungu achizimayi m’Nyumba ya Malamulo, Jessie Kabwila adati komitiyi iyambe yaona lamulo lomwe lapangidwalo ndi mfundo zake.

“Tione kaye mfundo zomwe zili mulamulolo n’kukambirana chifukwa mukomiti mumakhala anthu amaganizo osiyanasiyana. Ena amakhulupirira kuti kuchotsa mimba n’kupha pomwe ena amazitengera paufulu wa anthu ndiye mpofunika titagwirizana chimodzi ngati komiti,” adatero Kabwira.

Iye adati kupatula kusemphana maganizoku, nkhani yochotsa mimba njofunika kuyiona bwino chifukwa amayi ambiri akutaya miyoyo yawo tsiku ndi tsiku kaamba kochotsa mimba.

Mneneri wa polisi m’dziko muno Rhoda Manjolo adati imfa zokhudzana nkuchotsa mimba zikuchuluka akatengera m’mabuku a kupolisi.

Iye adati malingana ndi kafukufuku wa polisi, ambiri mwa amayi ndi asungwana omwe amachotsa mimba amachita izi kaamba ka mantha kapena kukhumudwitsidwa ndi omwe adawapatsa mimbazo.

Related Articles

Back to top button
Translate »