Nkhani

Lekani kulozanalozana, nyengo yasintha—MET

Listen to this article

Nthambi yoona za kusintha kwa nyengo ya Malawi Meteorological Services (MET) yati anthu adziwe kuti nyengo ikusintha ndipo aleke kulozana zala chifukwa palibe akuchititsa izi.

Mkulu wa nthambiyi Jolamu Nkhokwe adalankhula izi Lachitatu pamene nthambiyi imakumbukira tsiku la zanyengo.

Zikavuta choncho m’munda ena amaloza chala anzawo
Zikavuta choncho m’munda ena amaloza chala anzawo

Nkhokwe adati nthambi yawo nthawi zonse imapereka uthenga wa momwe nyengo ikuyendera, koma akudabwa kuti ena akukhalabe moyo wachikale womaloza ena zizindikiro za kusintha kwa nyengo zikaoneka.

“Ambiri sakudziwabe kuti pali kusintha kwa nyengo, dziwani kuti nyengo yasintha ndipo izi zikuoneka kudzera m’njira zambiri monga kusowa kwa mvula ndi kusefukira kwa madzi.

“Anthu agwiritsire ntchito uthenga womwe tikuwapatsa kuti atsatizire bwino za kusintha kwa nyengo. Tsiku lililonse tikumatulutsa uthenga wa momwe nyengo ilili koma tikudabwa kuti ena akukhala moyo wachikale,” adatero Nkhokwe.

Kulankhula kwa Nkhokwe kukudza pamene m’dziko muno anthu okalamba akukwapulidwa, ena kuwapha kumene powaganizira kuti akutseka mvula.

Ku Chiradzulu mwezi wathawu ndiye anthu 7 adaothetsedwa moto masanasana ndipo adawasiya atalonjeza kuti mvula ibwera.

Nkhoswe adati izi ndi zachisoni chifukwa palibe amene angatseke kapena kumasula mvula ndipo wapempha anthu kuti azitsatira zomwe nthambi yawo ikutulutsa kukhudzana ndi momwe nyengo ikhalire.

Malawi ndi limodzi mwa maiko amene akhudzidwa ndi kusintha kwa nyengo moti mvula chaka chino yagwa mwanjomba kupangitsa kuti ena asaphulemo kanthu m’minda yawo.

Related Articles

Back to top button