Chichewa

Leo Mpulula: Alibe 2 koloko

Listen to this article

Akulu, ligi ikuyamba, inu ngati kochi wa Max Bullets mwakonzeka bwanji?

Tapimana ndi matimu ambiri, zikuonetsa kuti anyamata agwira ntchito momwe ndikufunira.

Mudasewera ndi Wanderers, masewero adali bwanji?

Adali bwino, anyamata akuonetsa kulimba mtima, kusonyeza kuti ntchito igwirika.

Masewero atatha, mudawayankha atolankhani zamwano, vuto lidali chiyani?

Mpulula: Ndazitaya
Mpulula: Ndazitaya

Amwene, si mwano, koma atolankhani ena amadabwitsa. Adandifunsa kuti anyamata anga sadamenyere pagolo chifukwa chiyani. Ndiye ndidamufunsa kuti Wanderers idamenyera pagolo? Yekha adaona, ndiye amafuna chiyani? Amafuna timu ithe kapena?

Nanga bwanji apapa mwandiyankha momwe masewero adathera?

Inu kudalibe, komanso mtima wanga wakhala pansi ndipo ndapeza chomwe chidavuta, koma mudakandifunsa komweko ndiye mudakaona kuti ndi mwano koma chili chilungamo.

Mukafunsidwa momwe masewero mwawaonera, nthawi zonse mumabweza funso, pali vuto kodi?

Akandifunse momwe ndawaonera? Iyeyo adali kuti? Ndipo ngati iyeyo adaonera, bwanji osakalemba zomwe waonazo? Ndimabweza chifukwa si funso ayi. N’chimodzimodzi kumafunsa kuti madziwa akupezeka bwanji kubafaku. Ine ndiye ndiziti chiyani? Akudziwa kuti timu sili bwino, ndiye akufunsa kuti ndaiona bwanji? Iyeyo adali kuti? Akufuna chiyani? Yankho ali nalo koma akufunsanso, ndiye akufuna chiyani, amwene?

Amwene, koma ndamva kuti mwazitaya ku Max Bullets, zoona?

Kwambiri kwake. Ndazisiya. Amwene, mwini wake wa Max Bullets, Max Kapanda, samva za munthu ndiye ndangoti khala nayo timu yakoyo, ndapita.

Nkhani yake?

Ndinamuuza kuti apereke ma contract abwino kwa ma players koma iye amati player aliyense asayinire K100 000 kwa zaka zitatu, zoona zimenezo? K100 000 ndi chiyani kwa player wa mu Super League, si salale ya pamwezi imeneyo? Ndiye ma players amene ndimafuna anakana kusayinira K100 000 ndipo anapita ndiye inenso ngati kochi ndinangoti ngati ma players apita ndiye nditsala ndi nda? N’chifukwa chane nane ndachoka ku Max Bullets. Ubwino wake sindinasayine contract.

Mumalawako kapena, amwene?

Ine sindimwa mowa, ndimapemphera ku Chilobwe Church of Christ. Ndidasiya kumwa mowa 2005, mpingo wanga umandidalira, n’chifukwa chake ndili wakhalidwe. Momwe ndimalankhulira ndi momwemu, kungoti chilungamo ndi mwano zidayandikana, ukamanena chilungamo amati ndi mwano. n

Related Articles

Back to top button
Translate »