Nkhani

Likwata: Amuna aimba ng’oma, amayi navina

Listen to this article

Likwata ndi mmodzi mwa magule amene amavinidwa pakati pa Ayao. BOBBY KABANGO adali m’boma la Chiradzulu m’mudzi mwa Njeremba kwa T/A Mpama komwe adapezerera gule wa likwata, yemwe ena amamutcha kuti namkwakwala. Uyutu ndi gule amene amavina amayi komanso atsikana. Kodi uyu ndi gule wanji? Nanga adayamba liti? Mtolankhani wathuyu adakokera pambali mayi amene amatsogolera guleyu. Adacheza motere:

Eee! Wefuwefu ameneyu kutopa kumene?

Hahaha! Padalitu ntchito pamene paja. Si maseweratu kuvina gule ameneyu chifukwa akafika pakolasi timayenera tidzipinde basi.

Tidziwane kaye.

Ndine mayi Idesi Chiwaya, ndipo ndipo ndimatsogolera gululi.

Kodi ndi gule wanji ameneyu?

Ameneyu ndi gule wa namkwakwala, ena amati likwata.

Cholinga cha guleyu n’chiyani?

Kusangalatsa anthu basi. Timavina tikasangalala monga zachitikira leromu kuti tangosangalala ndiye tidakumana kuti tivine basi anthu adyetse maso.

Muli akazi okhaokha bwanji?

Ameneyu ndi gule wa amayi, nchifukwa chake simudaonemo mwamuna kupatula awiri amene akutiimbira ng’oma.

Ndaonamonso tiasungwana, timeneti timaloledwanso kukhala m’gulumu?

Eya, amenewo ndiye eni gululi chifukwa ife takulatu ndiye timakhala nawo kuti Mulungu akatitenga iwowo ndiwo adzatsogolere gululi. Sitikufuna kuti gule ameneyu adzafe.

Kodi guleyu saphunzitsa zoipa?

Zoipa zanji? Ayi, ameneyutu ntchito yake ndi kusangalatsa anthu basi.

Simukuona kuti guleyu angapangitse kuti tianamwali tija tisodzedwe mwachangu?

Hahaha! Musandiseketse inu, amene aja ndi adzukulu anga. Ndimawayang’anira ndipo palibe angachite zopusa ndi ana amenewa. Akukula m’manja mwanga.

Dzina limeneli lidabwera bwanji?

Dzina la guleli? Liti lomwe mukukamba?

Ndikukamba la likwata…

Ndi dzina basi, kusonyeza gule wachikhalidwe pamene ena amati gule wa namkwakwala.

Chifukwa chiyani kulipatsa dzina la ‘likwata’?

Basi, nawonso makolo adakonda kuti apereke dzinali.

Si zolaula zimenezi? Nanga mpaka likwata?

Ayi, palitu maina a anthu ambirimbiri m’dziko muno omveka ngati akulaulanso, kodi ndiye kuti anthuwo amachita zomwe dzinalo limatanthauza? Ife mukanena kuti likwata timatanthauza kuti ndi gule wosangalatsa basi.

Kodi ndi gule wa chikhalidwe chiti cha anthu?

Uyu ndi gule wa Anyanja. Ambiri akhala akunena kuti ndi wa Alhomwe, koma zoona zenizeni ndi zomwe ndikunenazi.

Mavinidwe a guleyu andimaliza, tafotokozani momwe muchitira pamene mukuvina…

Ng’oma ija ikamalira, ife timavina moitsatira uko tikuimba nyimbo zathu. Ndiye ikafika pakolasi, timachita ngati tikudumpha uko tikudula chiuno. Apa ndiye timagwadirira pansi ndi kuvina momatembenuka koma kumatembenuka ndi maondo kwinaku tikugundana ndi matako. Aka ndiye kavinidwe kake.

Adakuphunzitsani ndani?

Makolo athu. Ineyo makolo anga ankavina kwambiri ndipo atamwalira ndidapitiriza mpaka kupeza amayi anzanga. Tonse tilipo 10 kuphatikizapo ndi abambo a ng’oma takwana 12.

Abambo savina nawo chifukwa chiyani?

Aaa! Inuyo mungakwanitse zomwe timachita zija? Eetu, nchifukwa timavina amayi okha.

Mudayamba liti kuvina guleyu?

Chaka ndiye sindingakumbuke koma ndimakumbukira kuti panthawiyo ndidali ndi zaka 33. Pano zaka zanga ndidaziiwala koma zaposa 50.

Mumavina nthawi yanji?

Timavina masana, moti nthawi zambiri timavina pazochitika monga pamisonkhano. Tavinirapo mtsogoleri wakale Bakili Muluzi komanso Bingu wa Mutharika.

Atsogoleriwa amakwanitsa kuduka m’chiuno chonchi?

Ayi, amangochoka pampando ndi kumavina pang’onopang’ono ndipo mapeto ake amapisa m’thumba kutipatsa kangachepe.

Kodi momwe munavinira apamu ndiye kuti mumathera pamenepa?

Ayi, apatu tangovina kwa mphindi 5, koma tikati tivine moposera mphindi zimenezi mudakaona momwe timachitira.

Malangizo kwa amene satsatira gule wa makolo…

Amenewo azikhala pafupi ndi makolo awo kuti asataye chikhalidwe cha makolo awo.

Related Articles

Back to top button