Chichewa

Lingalirani zobzala mitengo

Listen to this article

 

Mvula masiku ano ikugwa mwanjomba, kutentha kukuonjeza, madzi sachedwa kuuma komanso nthaka ikukokoloka modetsa nkhawa. Awa ndi ena mwa mavuto omwe akatswiri akuti akudza chifukwa chilengedwe chikuonongedwa ndi kusasamala makamaka mmene anthu akudulira mitengo. Chaka ndi chaka m’dzinja, Amalawi amalimbikitsidwa kubzala mitengo pofuna kubwezeretsa chilengedwe. STEVEN PEMBAMOYO adacheza ndi mkulu wa bungwe la mgwirizano wa alimi la Farmers Union of Malawi (FUM) Prince Kapondamgaga zokhudza ntchitoyi.

 

Kodi a Kapondamgaga nchifukwa ninji masiku ano nyengoyi ikuoneka kuti siikupanganika?

Pamenepa anthu akhoza kuzungulirapo kwambiri koma nkhani yeniyeni ndi yakuti anthu adaononga chilengedwe kwambiri ndiye momwe zinthu zimayendera kale si momwe zingamayenderenso panopa ayi.

Mukutanthauzanji pamenepa?

Kapondamgaga kubzala mtengo chaka chatha
Kapondamgaga kubzala mtengo chaka chatha

Apa ndikutanthauza kuti momwe mvula inkagwera kale si momwe ingagwerenso pano chifukwa mwachitsanzo tonse tikudziwa kuti mvula imabwera chifukwa cha mitengo yomwe imasefa mpweya malingana ndi mmene zimakhalira mlengalenga. Panopa mitengo ija idatha ndiye mpweyawo usefedwa bwa?

Nanga ngati mpweya si usefedwa, mvula ichokera kuti?

Mukakamba za kutentha ndiye musachite kufunsa chifukwa mpweya wotentha omwe anthu ndi zinyama komanso mafakitale zimatulutsa, mitengo imayamwa nkumapangira chakudya ndipo imatulutsa mpweya womwe timapuma nkumanyadirawu koma tsopano mitengoyo kulibe nchifukwa chake kumatentha motere.

Ndiye inu mwati alimi azibzala mitengo yambiri, ndiye kuti nkhani ya mitengoyi imakhudza alimi okha?

Ayi, si ntchito ya alimi okha koma munthu aliyense kungoti ambiri mwa mavuto omwe tatchulawa akukwapula kwambiri ntchito za ulimi. Chifukwa cha kutha kwa mitengo, nthaka lero ili pamtetete zomwe zikuchititsa kuti mvula ikangogwa ngakhale pang’ono, madzi azithamanga kwambiri nkumakokolola nthakayo moti pano chonde chambiri chidapita.

Ndiye mwati njira yake nkubzala mitengo basi?

Basitu ndiye njira yake imeneyo. Komanso sikuti kubzala mitengoko ndiye kuti mukukonza kapansi muulimi okha ayi chifukwa pali ntchito zambiri za mitengo monga kutchisira fodya kwa alimi a fodya, kumangira zigafa, kuchita mapaso a nyumba, kupangira mosungira zokolola monga nkhokwe, kumangira makola a ziweto, nkhuni ndi ntchito zina zambirimbiri.

Kodi mitengoyo ikhoza kubzalidwanso mwa mthirira?

Palibe vuto bola ngati munthu ali ndi madzi komanso nthawi yothirira mitengoyo koma nthawi yabwino ndi nyengo ya mvula nchifukwa chake chaka ndi chaka nyengo ya mvula kumakhala nyengo yobzala mitengo. Nyengoyi ndi yabwino chifukwa kuthirira kwake nkosavuta madzi amakhala ambiri, ntchito imakhala yongolambulira basi. Mvula ikamadzati ikutha, mitengo yambiri imakhala itagwira moti siivuta chifukwa munthu akhoza kukhala sabata zingapo osathirira koma mitengo osafa.

Kodi mitengoyo nkungobzalapo kuti bola mitengo kapena bwanji?

Ayi ndithu mpofunika kuona posankha mitengo yobzala. Kusankha kumatengera ndi malo ake monga pali mitengo ina yoteteza ku mphepo ya mkuntho yomwe imafunika kukhala yamizu yozama kuti izipirira ku mphamvu ya mphepoyo. Palinso mitengo ina yoteteza nthaka yomwe imafunika kukhala ya mizu yoyanza bwino kuti madzi asamathamange kwambiri. Koma pankhani ya ulimi timalimbikitsanso kubzala mitengo yachonde yomwe alimi angakambirane ndi alangizi m’madera mwawo.

Mlimi wamba angapeze bwanji mbande za mitengo?

Eya, pali njira zambiri zopezera mbande za mitengo. Njira yoyamba ndi kugwirizana pamudzi nkuona vuto lomwe lilipo ndipo mukatero mukhoza kukauza alangizi kuti akuthandizeni komwe mungapeze mbande. Njira yomweyo mukhoza kupanga pakalabu kapena munthu aliyense payekha. Kutengera upangiri wa alangiziwo, mukhoza kuona kuti muchita bwanji chifukwa pali mbande zina zomwe alimi ena amafesa nkumagulitsa zomeramera komanso mukhoza kungogula mbewu kapena kutola m’nkhalango nkufesa nokha kuti pofika nyengo ya mvula mudzakhale ndi mbande.

Inuyo a bungwe la mgwirizano wa alimi mumatengapo mbali yanji pantchitoyi?

Ifeyo ndi amodzi mwa magulu omwe ali patsogolo kulimbikitsa ntchitoyi moti chaka chilichonse timakhala ndi tsiku lomwe timakabzala mitengo kumalo ena ake malingana ndi pologalamu yathu. Kupatula apo, timakhalanso tikubzala mitengo patokhapatokha m’madera momwe timakhala komanso alimi ndi mabungwe ena akatiyitana kuti tikakhale nawo akakonza mwambo wobzala mitengo ife timakhala okonzeka.

Nanga monse tidayambira kubzala mitengo muja siidakwanebe?

Ambuye musadzakhale ndi maganizo amenewo. Mmene anthu akudulira mitengomu mungamati yobwezeretsapo yakwana zoona? Ndiponso kunenna mosapsatira pakufunika kubzala mitengo yambiri zedi kuyerekeza ndi yomwe imabzalidwa chaka ndi chaka. Osayiwalanso kuti mitengo yomwe imabzalidwa siyonse yomwe imakula; ina imafa ndiye imafunika kubwezeretsa.n

Kapondamgaga kubzala mtengo chaka chathandiwo akulima.

 

 

 

 

Related Articles

Back to top button