ChichewaEditors Pick

Lonjezo la jb Lasanduka loto

Listen to this article

 

Bambo ake adamwalira, chiyembekezo chidali pa bambo womupeza, nawonso adamukhumudwitsa pomugwiririra n’kumupatsa pathupi ndipo bwalo la milandu lidamugamula kuti akaseweze kundende zaka 13. Moyo wakhala wowawitsa; loto lodzakhala wapolisi lidasanduka la chumba.

Koma pa 18 March 2013, chiyembekezo cha Zione (tangomupatsa dzinali) chidatukusira pamene yemwe adali mtsogoleri wa dziko lino Joyce Banda adamulonjeza kudzamulipirira maphunziro ake mpaka kuyunivesite.

Malinga ndi mphunzitsi wa Zione, Dziwa Nazombe-Mbewe, Banda adalonjeza Zione patsiku lomwe amayendera ku One-Stop-Centre kuchipatala cha Queen Elizabeth Central mumzinda wa Blantyre.

“Patsikulo ogwira ntchito ku One Stop Centre adandiimbira kuti apulezidenti akhala akuyendera malowo ndiye akufuna Zione akalankhule zomwe zidamuchitikira.

“Ndidapita naye ndipo apulezidenti adafika m’chipinda chathu momwe adacheza ndi Zione yemwe panthawiyo adali ndi zaka 13. Atamufunsa za sukulu, iye adati akufuna apitirize. Apa mpamene apulezidenti adati amulipirira sukulu yake,” adatero Nazombe-Mbewe.

Tsogolo sakuliona: Zione (kumanzere) ndi aphunzitsi ake Mayi Nazombe-Mbewe
Tsogolo sakuliona: Zione (kumanzere) ndi aphunzitsi ake Mayi Nazombe-Mbewe

Iye adati Banda adauza mayi Lingalireni Mihowa amene adali nawo panthawiyo kuti ndiwo azilumikizana nawo pankhani ya thandizolo.

Chimwemwe chidadza ngati mmawa kwa Zione, zoti adachitidwa chipongwe ndi bambo ake, zidaiwalika. Tsopano loto lodzakhala wapolisi lidayamba kuoneka tsogolo lake.

“Ndidali ndi chimwemwe. Titangotuluka, ndidaimbira foni malume anga ku Balaka komanso kudziwitsa anzanga akusukulu zomwe apulezidenti adandilonjeza, ndidasangalala kwambiri,” adatero Zione.

Chidatsala nkuti Zione, yemwe panthawiyo adali Sitandede 8, akhoze mayeso. “Ndidakalimbikira kusukulu ndipo ndidakhozadi,” adatero.

Apa mpamene mphunzitsiyu adakambirana ndi Mihowa kuti Zione akalowe Fomu 1 kusekondale.

“Ndidapita kuofesi kwawo ndipo tidakambirana poti panthawiyo nkuti Zione adali asadabereke, adati tidikire abereke kaye kuti abwerere kusukulu,” adatero Nazombe-Mbewe.

Pa 9 January 2014, mwana adabadwa ndipo ati adagwirizana kuti pakatha miyezi 7 Zione akayambe sukulu. Mu July mwana adamuleketsa kuyamwa kuti abwerere kusukulu.

Nazombe-Mbewe adayesera kutsatizira nkhaniyo koma sinaoneke mutu wake.

“Ndidapita kuofesi kwawo ndipo adati andiimbira. Poona kuti sakuimba, ndidapitanso ndipo adandiuza kuti ndisiye nambala aimba, koma sadaimbe. Ndidadzapitanso pamene adati ndilembe nkhani ya Zione ndipo aitsatizira koma sizidatero mpaka lero pamene ndatopa,” adatero Nazombe-Mbewe.

Ngakhale mphunzitsiyu adalembera ofesi ya Mihowa kalata zokumbutsa za lonjezolo, komabe palibe chidachitika mpaka lero.

Msangulutso utaimbira foni Mihowa, iye adati tilankhule ndi Levi Mwase amene amayendetsa nkhaniyo. Koma Mwase adati “sindine mneneri wa Joyce Banda, imbirani mneneri wake Tusekere Mwanyongo”.

Mwanyongo adati nzovuta kuti anene chifukwa chenicheni chomwe lonjezolo silidatheke koma wati mwina padalibe kulumikizana kwabwino.

“Mayi Joyce Banda akhala akuthandiza ndipo mpaka lero akuthandizabe ana ambiri asukulu. Nkutheka kuti padalibe kulumikizana kwabwino ndi mtsikanayo,” adatero.

Koma mthandizi wa Banda, Andekuche Chanthunya, akuti ndondomeko zoyenera sizidatsatidwe n’chifukwa mtsikanayu sadathandizidwe.

“Samayenera apite kwa Mihowa koma abwere kwa ine kapena kwa Levi [Mwase]. Ngati akufuna kuthandizidwa akuyenera atsatire ndondomeko,” adatero.

Njovu zikamamenyana udzu ndiwo umavutika. Kuponyerana Chichewaku sikukuthandizabe Zione amene pano akusungidwa ndi banja lina ku Chirimba mumzinda wa Blantyre.

Banja lomwe likusunga Zione silingakwanitsenso kumutumiza kusukulu. Bambo wa pabanjapo, Evance Milanzie wati moyo wa Zione wafika pomvetsa chisoni.

“Ndi mwana wanzeru, zangovuta kuti lonjezolo silidatheke,” adatero Milanzie.

Aka si koyamba kuti mtsogoleri wa dziko alonjeze mwana koma osakwanitsa lonjezolo. Mu 2004, mtsogoleri wakale Bingu wa Mutharika adalonjezanso Marietta Mhango wa m’mudzi mwa Mawelera kwa Paramount Kyungu m’boma la Karonga kuti adzamulipirira sukulu.

Mutharika adalonjeza Marietta pamsonkhano kuti adzamulipirira atanena bwino ndakatulo, koma ngakhale adatsindika za thandizolo, izi sizidatheke ndipo lero Marietta akutuwa.

Kodi izi zimatero chifukwa chiyani?

Mphunzitsi wa zandale kusukulu ya Chancellor Collage Joseph Chunga akuti mtima wofuna awaone ndi omwe umachititsa.

“Amafuna kuti mwina aoneke kuti ali ndi mtima wabwino, cholinga akalonjeza apateko mavoti chifukwa cha mtima womwe aonetsa, koma n’zachisoni,” adatero Chunga.

Pamene izi zili chonchi, Zione ndi wokhumudwa ndipo zasokoneza moyo wake. Katswiri kumbali ya kaganizidwe ka munthu, Chiwoza Bandawe akuti Zione kukhala wachichepere, izi zingakhudze moyo wake.

“Sindinganene bwinobwino kuti zimukhudza bwanji chifukwa nkhani iyi ikufunika kukumana naye. Zambiri ndinganene nditamuona,” adatero Bandawe. n

Related Articles

Back to top button
Translate »