ChichewaEditors Pick

Luso losema ziboliboli

Listen to this article

Luso longosema lafika apa?

Basitu ntchito zake Namalenga kuti nafenso tikhale ndi popezera ndalama.

Malo anu amenewa?

Amenewa ndi malo anga komanso mkulu wanga amene  ndikugwira naye ntchitoyi.

Mudatsegula liti malo ano?

Alick kuonetsa chipembere chomwe adasema

Adatsegulidwa mu 2012, koma ndidayamba kusema ziboliboli mu 1998.  Nthawiyo ndimagwira ntchitoyi ndikukhala ku Mua kenaka ndimapangira kunyumba kwanga. Mu 2012 ndi pamene timatsekula malo ano.

Mumasema chiyani?

Timasema mtundu ulionse wa zinyama omwe munthu akufuna, chifaniziro cha munthu, mayi Maliya, chifaniziro cha anthu a mtundu wa Chingoni, galimoto ndi zina zambiri zomwe sindingakwanitse kuzitchula zonse.

Mukugwiritsa ntchito mtengo wanji?

Pali mitengo yambiri yomwe anthu amagwiritsa ntchito koma ife timakonda mtengo wa mtumbu.

Mumagwiritsira zida ziti popanga katunduyu?

Mukakadula mtengowo, mumayenera kuyamba kusema ndi sompho, chikwanjenso chimafunika, tchizulo, sandpaper, polish ndi zida zina ndi zina kuti chomwe tikusemacho chioneke bwino.

Ndaona chifaniziro cha nyama ya chipembere, zimatenga masiku angati kuti mupange? Nanga mumagulitsa bwanji?

Pakutha pa sabata ziwiri timakhala tamaliza kupanga chipembere. Chimenechi chikugulitsidwa K15 000. Chifaniziro cha mayi wa mtundu wa Chingoni timagulitsa K20 000.

Kodi lusoli ndi lokatamutsa?

Ndagula nyumba,  ndimalipirira ana sukulu komanso feteleza ndimagula kuchokera m’ntchitoyi. Ichi ndi chisonyezo kuti muli ndalama ndithu. n

Related Articles

Back to top button