Lolemba lapitali, mafumukazi athu, ma Queens, adali ku nyumba yachifumu ya Sanjika mumzinda wa Blantyre kumene mtsogoleri wadziko lino Peter Mutharika adawaitana ku nkhomaliro. Izi adachita pofuna kuwathokoza pantchito imene adagwira mumpikisano wadziko lonse wa Fast5. Iwo adali panambala 3. Mtsogoleri wa dziko linoyo adawapatsa asungwanawo mphatso ndi
K300 000 aliyense zimene asenza pachithunzipa.