Nkhani

Mabungwe ati boma likonze zinthu mu 2015

Kuphedwa kwa kwa wapolisi mumzinda wa Blantyre ndi kuvulaza wina komanso kuthyoledwa kwa mabanki ndi malo osiyanasiyana ndi chisonyezo kuti ng’ombe zayang’ana kungolo m’dziko muno.

Si zokhazo. Nkhani zoti apolisi ena adagwidwa akuchita umbanda ndi kuthyola mabanki sizikupereka chiyembekezo choti m’dziko muno muli chitetezo chokwana.

Ngakhale mkulu wa apolisi m’dziko muno, Paul Kanyama, akuti ntchito ili mkati yokonza chitetezo, izi sizikuoneka chifukwa nazo mbadwa za m’dziko la China zanenetsa kuti zinyamuka m’dziko muno ngati zophanazi zipitirire.

Ichitu ndi chitsanzo cha zonyansa zomwe zakhala zikuchitika mu 2014 kuti mpaka anthu lero adandaulire boma kuti likhwimitse chitetezo pamene talowa chaka chatsopano.

Sikuti ndi mtauni mokha, nako kumudzi akuti anthu akuyenda mocheuka kaamba ka ambanda amene akuba komanso kutibula anthu.

“Kuno kwaopsa achimwene, mmene mvula yayambamu, sungayende usiku, akupha apo ayi akubera,” adatero Rose Manuel wa m’mudzi mwa Jumbe, kwa Senior T/A Kachindamoto m’boma la Dedza.

Nako kumbali ya zaumoyo, anthu ati boma likonze zinthu chifukwa 2014 anthu amabwezedwa m’zipatala powauza kuti mankhwala kulibe.

Martin Dinesi wa m’mudzi mwa Ndalama, kwa T/A Nkalo m’boma la Chiradzulu, komanso Limbani Gondwe wochokera ku Mchengautuwa ku Mzuzu, ati kumudzi anamizidwa kwa nthawi kotero boma lichitepo kanthu.

“Kunoko zipatala n’zosakwanira, zomwe zimachititsa kuti anthu azithithikana, mapeto ake tikungopatsirana matenda. Mabedi ndi ochepa, mankhwala mulibenso. Izi zithe ndipo tione kusintha m’chaka chimenechi,” adatero Gondwe.

Mkulu wa bungwe la zaumoyo la Malawi Health Equity Network (Mhen) Martha Kwataine akuti mavutowa ali apo, chomwe chidadandaulitsa bungwe lawo mpamene unduna wa zaumoyo udalandira ndalama zochepa mundondomeko ya zachuma cha dziko lino.

Anthuwa adandaulanso umphawi womwe ati udanyanya m’chaka cha 2014. Koma malinga ndi katswiri pazachuma, Henry Kachaje, mavutowa avuta kuti athe kaamba ka masitalaka amene angoti mbwee m’dziko muno.

Kachaje akuti ngati boma likweze malipiro a anthu amene akuchita masitalakawa, ndiye kuti chuma chisokonekera chifukwa choti abwenzi a dziko lino sadasinthe maganizo awo kuti ayambe kuthandiza dziko lino.

“Abwenzi a dziko lino anenetsa kuti adzayambanso kuthandiza dziko lino pachuma pokhapokhapo litathana ndi nkhani za kubedwa kwa ndalama m’boma. Ichi ndi chisonyezo kuti mavuto akula msinkhu,” adatero Kachaje.

Patha miyezi iwiri tsopano ogwira ntchito m’bwalo a milandu akunyanyala ntchito pofuna kukakamiza boma kuti liwakwezere malipiro awo. Nawo a bungwe lothana ndi ziphuphu ndi katangare la ACB akunyanyalanso ntchito. Masitalaka ena akuchitika ku Kamuzu Central Hospital, College of Medicine ndi ku Chancellor College.

Nayo nkhani ya zaulimi ndi yomwenso yakwiyitsa anthu amene akupempha boma kuti sakufuna aonenso mavuto okhudza makuponi amene adawaona chaka chatha.

“Tikafunsa akutiuza kuti feteleza adatumiza kale pamene kuno sadafike. Zaka zonse timalira chonchi. Tatopa nazo ndipo tikupempha boma kuti lithane ndi vutoli,” adatero Christopher Julius wa m’mudzi mwa Musasa m’boma la Chiradzulu.

Koma mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika, polankhula muuthenga wa nthawi yachisangalalo cha Khrisimasi komanso chaka chatsopano, adati boma lake laponda giya pofuna kusintha zinthu.

“Kubedwa kwa ndalama m’boma kwakhudza mbali iliyonse. Komabe tikuyesetsa kuti tithane ndi mavutowa ndipo pakutha pa chaka chamawa tikhala titakonza zambiri,” adatero.

Related Articles

Back to top button