Nkhani

Mafumu asalidwa pogawa chimanga

Listen to this article

Ntchito yogawa chakudya kwa anthu osoweratu pogwira ili mkati koma kafukufuku wathu wasonyeza kuti mafumu sakukhutira ndi momwe ntchitoyi ikuyendera makamaka pa kasankhidwe ka anthu olandira chakudyachi.

Kafukufukuyu wapeza kuti mabungwe ambiri omwe akuthandizana ndi boma pa ntchitoyi akusankha okha anthu oti alandire chakudya ndipo nthambi yolimbana ndi mavuto ogwa mwadzidzidzi ya Department of Disaster Management Affairs (DoDMA) yati njirayi ichepetsa katangale.

Akuti midzi yambiri  yasiyidwa: Lukwa
Akuti midzi yambiri yasiyidwa: Lukwa

Mmbuyomu, mbiri ya ntchito yogawa chakudya kapena zipangizo zina m’midzi pogwiritsa ntchito mafumu ndi makomiti a m’midzi idada ndi nkhani ya katangale pa kasankhidwe ka anthu olandira.

Koma mafumu auza Tamvani kuti njira yomwe ikutsatidwa tsopanoyi ndiyo ingapititse patsogolo katangale chifukwa anthu osayenera kulandira akhoza kupeza danga kaamba koti olembawo sakudziwa za mmadera.

“Tikungomva kuti anthu akulembedwa maina kuti akalandire chakudya kapena ndalama ife mafumu osatengapo mbali ndiye mapeto ake, anthu osayenera kupindula nawo akupezeka pamndandanda,” adatero Senior Chief Chapananga wa ku Chikwawa.

Mfumu yaikulu Chadza ya ku Lilongwe idati chifukwa choti anthu omwe akuchita kalemberayu sadziwa bwinobwino madera omwe akugwiramo ntchitowo, midzi yambiri ikudumphidwa kusiya anthu ambiri padzuwa.

“Anthu omwe akuchita kalembera sadziwa malire kuti adayenda bwanji kapena kuti kuli anthu ochuluka bwanji. Pachifukwachi, midzi yambiri ikudumphidwa; mwachitsanzo, m’dera langa lino, muli Senior Group Mwenda yemwe ali ndi mafumu 80 komanso anthu 6 000 omwe adumphidwa,” adatero Chadza.

Senior Chief Lukwa wa ku Kasungu adati mwa mafumu opitirira 200 a m’dera lake, mafumu 6 okha ndiwo alowa mukalembera wa anthu olandira chakudya kutanthauza kuti midzi yambiri yasiyidwa ndipo avutika.

Mfumu yaikulu Chindi ku Mzimba adati iye adangomva kuti anthu ena alembedwa maina ndipo kuti ena ayamba kulandira chakudya koma osadziwa komwe zikuchokera ndi momwe zikuyendera.

“Adalembana okha komweko ife sizidatikhudze ayi komanso zoti anthu akulandira chakudya tikungomva. Mwachitsanzo, ndidangomva mphekesera kuti cha ku Edingeni anthu adalandirako chimanga koma ndilibe umboni,” adatero Chindi.

Mneneri wa nthambi ya Dodma Jeremiah Mphande adati njira yomwe ikugwiritsidwa ntchito posankha anthu ndiyamakono komanso yothandiza kuchepetsa chinyengo ndi katangale yemwe adalipo kale.

Njirayi yomwe akuitcha Unified Beneficiary Registry (UBR) imatenga kaundula wa anthu ovutika nkuwayika m’magulu potengera mavutikidwe awo ndipo kuchoka apo amazindikira thandizo loyenera kupereka ku maguluwo.

“Kuchoka pa mndandandawu, amthandizi pakhomo, amatengapo anthu awo, a ntchito za chitukuko amatengaponso ndipo ofunika thandizo la chakudya nawo amachoka momwemo. Njirayi imachepetsa kulakwitsa kowonjezera kapena kuchotsera anthu mu kaundula,” adatero Mphande.

Malingana ndi DC wa m’boma la Lilongwe, Charles Makanga, bomali lidatsatadi njira yatsopano pofuna kuthetsamavuto ena omwe adalipo m’njira yakale monga kulowetsa ndale za pamudzi mupologalamu.

“Chomwe chimachitika mundondomeko yakale nchakuti mafumu amayenera kugwirira ntchito limodzi ndi makomiti monga Village Development Committee (VDC) ndi Area Development Committee (ADC) koma pamakhala kuyendana m’mbali.

“Tili ndi zitsanzo zambiri zomwe kumapezeka kuti mfumu payekha walemba maina kapena anyamata ena a mukomiti alemba maina kwa okha ndiye zimasokoneza pologalamu,” adatero Makanga.

Related Articles

Back to top button