Nkhani

Mafumu ayamikira kuyamba kwa ziphaso

Mafumu m’dziko muno ati kuyamba kwa ntchito yopanga ndi kupereka ziphaso zosonyeza unzika, ndi chiyambi chopititsa patsogolo ntchito za chitukuko zosiyanasiyana kaamba koti ndi njira imodzi yotsekera mang’a a katangale.

Dzana Lachinayi, mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika adatsegulira ntchitoyi mumzinda wa Lilongwe ndipo pomva maganizo a mafumu, Tamvani idapeza kuti ntchitoyi ikomera mtundu wa Amalawi.

Kachindamoto: Tikuyamika
Kachindamoto: Tikuyamika

Mwa zina, mafumu adati zitupazi zithandiza kuti mchitidwe woba mankhwala m’zipatala, kutulutsa ndi kulowetsa katundu mwachinyengo, kuthithikana m’misika ndi maukwati osalongosoka zichepe.

“Timadandaula usana ndi usiku, chaka ndi chaka kuti mankhwala samalimba m’chipatala cha Dedza. Si kuchipatala kokha, ayi, komanso ku Admarc kokagula chimanga ndi kuthithikana m’misika chifukwa chosazindikirana.

“Ambiri mwa anthu omwe amapindula ndi ochoka kunja kaamba koti pozindikira kuti akuchita zachinyengo, amalawirira n’kukakhala oyambirira kulandira thandizo. Amalawi akamabwera amapeza mankhwala atha, malo mumsika atha ngakhalenso chimanga chimene ku Admarc chatha,” idatero mfumu yayikulu Kachindamoto ya m’boma la Dedza Lachinayi.

Mfumu yaikulu Mlauli ya ku Neno, komwe ndi kufupi ndi malire a Malawi ndi Mozambique kudzera ku Mwanza, idati mafumu kumeneko adali pachipsinjo chachikulu pankhani yokhudza milandu ya malo kaamba kamaukwati osadziwika bwino.

“Anthu amangochoka uko n’kudzafunsira mkazi kuno ndiye poti padalibe zitupa, kumakhala kovuta kuwazindikira bola akangodziwako midzi ingapo n’kumanamizira kuti amachokera kumeneko. Mapeto pake banja likavuta zimavuta kuweruza kwake ndipo akudza amapezeka kuti alanda malo,” adatero Mlauli.

Inkosi Khosolo, ya m’boma la Mzimba, idati chitupa n’chitetezo choyamba kwa munthu kaamba poti kulikonse angapite, anthu amatha kumuzindikira.

“Timachitira pangozi kapena munthu ukasowa kumene, ukakhala ndi chitupa, anthu amakuzindikira msanga n’kukuthandiza,” adatero Khosolo.

Related Articles

Back to top button