Mafumu ku Mwanza akwiya ndi Achewa

Anthu m’midzi ingapo m’boma la Mwanza akunyanyala ntchito zachitukuko pokwiya ndi ganizo la mfumu yayikulu T/A Kanduku loti Achewa m’dera lake ayambe kutsatira Chingoni.

 

Mafumu angapo komanso anthu ena afotokoza m’sabatayi kuti nacho chikhalidwe cha Achewa chili pachiopsezo.

Mwa zina, anthuwa ati Kanduku walamula kuti madambwe atsekedwe ndipo asadzamvenso gule akulira, ufumu wa Achewa usinthe kuti adziulonga mwa Chingoni ndipo osafuna izi akaone kokhala.

Iwo ati Kanduku adalamula izi miyezi isanu yapitayo.

Bwanamkubwa wa bomalo, Sumati Gwedemula, watsimikizira nkhaniyi ndipo wati adaitanitsapo Kanduku n’kumufunsa zingapo komanso kumulangiza za khalidwelo.

Kanduku adakana kulankhulapo pankhaniyi Lachitatu m’sabayi titamutchaira lamya, ati tifunse mfumu yaikulu ya Angoni, Inkosi Gomani ya ku Ntcheu.

Apa wogwirizira ufumu wa Gomani, Malinki Gomani, wati palibe cholakwika chifukwa anthuwa adakapalamula kwa Kanduku pomwe amamudzoza ufumu.

Koma Malinki sadafotokoze zomwe mafumuwo adapalamula. Iye wati ngati mafumuwo akufuna zinthu zibwerere chikale, akapepese kwa Kanduku.

Mkulu wa bungwe lachikhalidwe cha Achewa la Chewa Heritage Foundation, Mark Zililakhasu wati ndiodabwa ndi nkhaniyi chifukwa m’madera ena ambiri mitundu ingapo imakhala limodzi molemekezana.

Nduna yoona za maboma aang’ono, Henry Mussa, yati boma silingalole mchitidwewu.

Mussa wati boma likatsekula madambwewo komanso kumva kuchoka kwa Kanduku.

“Uku n’kulakwa. Sizingatheke boma kukhala mtundu umodzi,” adatero Mussa.

Nyakwawa ina komanso magulupu a m’dera la Kanduku omwe adati tisawatchule maina afotokoza m’sabatayi kuti chitukuko chalowa pansi m’madera awo chifukwa anthu awo tsopano akunyanyala ntchito zachitukuko pokwiya ndi ganizo la Kanduku.

Ntchitozi ndi monga kulambula misewu.

Ofotokozawo ati Kanduku-yemwe ali ndi mafumu 77-adaitanitsa mafumuwa mu Okutobala chaka chatha ndikuwauza kuti m’dera lake sakufunanso Achewa.

Apa akuti adalamula kuti sakufunaso kumva gule wamkulu akulira m’dera lake, apo bii mfumu ya m’mudzi wolola gululewo idzalipa ng’ombe kwa mfumu yaikulu ya Angoni, Inkosi Gomani.

Malinga ndi mafumu odandaulawa, Kanduku adanenetsa kuti ulamuliro umenewo udachokera kwa Inkosi Gomani.

Mafumuwa ati Kanduku adanenetsa kuti yemwe akufunabe mwambo wa Achewa asamukire komwe kuli Achewa.

Apa iye adalamula mafumuwa kuti agule zachingoni monga mthini, mnyoni, chibonga, mkondo, chishango, ndi zibiya komanso nsalu zokhala ndi mauthenga ndi zizindikiro za Chingoni.

Mafumu anayi adaonetsa Tamvani zovala zachingoni zomwe tsopano ali okakamizidwa kuvala.

Lachiwiri m’sabatayi, motsogozedwa ndi akulu ena a dambwe, Tamvani idayendera madambwe otsekedwa a midzi ya Kunenekude, Liwonde, Siledi, Msakambewa, Eliya ndi Mchotseni.

Madambwe ena asanduka minda pomwe ena awirira.

Lachitatu, Tamvani itadziwitsa Gwedemula za madambwe otsekedwawo kudzera pa lamya, iye adali wodabwa chifukwa ati adalamula Kanduku mkati mwa chaka chatha kuti atsekule madambwe otsekedwawo.

“Ndidauzanso mafumuwa kuti anene komwe kwatsekedwa madambwe, koma sadandiuze. Zakhala bwino kuti mwandidziwitsa; ndiona momwe ndichitire,” adatero bwanamkubwayu.

Gulupu wina yemwe dera lake muli mabanja oposa 11 000, wati chaka chilichonse pofika mwezi wa Febuluwale amakhala atamaliza chitukuko cholambula misewu isanu ndi umodzi (6) m’deralo, koma mpaka lero sadayambe ndi msewu umodzi womwe.

“Anthu akukana, tikawaitana akumati tawaphera chikhalidwe chawo kotero ngati tikufuna kuti abwere titsekule madambwe.

“Pa lero tili ndi chitukuko chomanga malo ochitira msonkhano komanso kulambula msewu. Patsiku lachitukuko amabwera anthu oposera 400 koma lero kwabwera amayi 30 ndi amuna osaposa 10,” adatero Gulupuyu.

Iye adati ali ndi mantha kuti chikhalidwe chawo chisokonekera komanso padzikhala kukangana polowa ufumu chifukwa chakusintha komwe kwadza.

“Ine ndi Mchewa ndipo ndimatsata gule. Pachikhalidwe chathu, wolowa ufumu ndi chidzukulu.

“Koma pachingoni, wolowa ufumu ndi mwana wako. Namwali akatha msinkhu akuti tidziwauza kuti aitanitse angoni akwa Gomani kuti adzamuvinire kapena tidzimutumiza kwa Gomaniko kuti akamuvinire,” adatero Gulupuyo.

Iye adati mafumu Achichewa adapempha kuti ngati pena pakulakwika auzidwe kuti akonzepo, koma sadauzidwe kanthu, kotero lero akungomvera lamulolo chifukwa ali mkhwapa mwa Kanduku.

Nyakwawa ina yati kusinthaku kwabwera ndi Kanduku yemwe adalongedwa m’chaka cha 2010. Nyakwawayi yati m’mudzi onsewo, momwe muli mabanja 300, mabanja awiri okha si a Achewa.

Iyo idati tsopano anthu akukana kupita kuchitukuko.

“Tikumanga buloko yasukulu komanso nyumba ya mphunzitsi ndiye banja lililonse likupereka K500, kufikira lero patha miyezi itatu koma mabanja asanu okha ndi amene apereka; ambiri akukana pofuna chikhalidwe chawo,” idatero nyakwawayi.

Yohane Gumbwa, yemwe ndi mkulu wa dambwe wati pali mantha kuti mizimu iwakantha chifukwa chosiya mwambo wawo.

Iye adati pamaliro gule wamkulu amayenera avine, chimodzimodzi pamatenda ndipo kudambwe sikuyenera kukhala kosalowedwa.

“Ngati maliro apita osavinira, mizimu ya malemuyo imavutitsa abale ake, mwinanso anthu kumangopululuka. Ndasiya kupita kuchitukuko mpaka madambwe atatsekulidwa,” adatero Gumbwa.

Koma Malinki watsutsa madandaulo angapo omwe mafumu kwa Kanduku ali nawo.

Iye wakana zoti pali ganizo loti anamwali akatha msinkhu azitumizidwa kwa iye.

“Ufumu ulipowo ndi wachingoni ndiye mafumu onse omwe ali m’deralo akuyenera azichita zachingoni.

“Amayenera adzivala zachikhalidwe chachingoni monga m’misonkhano ndipo izi sizachilendo,” idatero Inkosiyi.

T/A Kanduku watsopanoyu, yemwe dzina lake lakubadwa ndi Helemesi Moliyo Kanduku, adalowa ufumuwu kutsatira kumwalira kwa bambo ake, Moliyo Kanduku.

Bomali lili ndi anthu oposera 80 000 ndipo muli Angoni, Amang’anja, Ayao, Achewa ndi Asena.

Zomwe zasintha

• Ofuna za Achewa akaone kokhala

• Madambwe atsekedwe, gule asalirenso

• Achewa adzilonga ufumu mwa Chingoni

• Mafumu onse adzivala zachingoni

• Anthu akunyanyala chitukuko pofuna chikhalidwe chawo

Share This Post