Nkhani

Mafumu okwezedwa ndi JB ali padzuwa

Listen to this article

Zasolobana kumpando wa chifumu pamene mafumu ena atsopano amene adakwezedwa ndi mtsogoleri wakale Joyce Banda ayamba kuona mbonawona.

Tikunenamu, mafumu akuluakulu ena alembera boma kuti lichotse mafumuwa poti adakwezedwa ndi kulongedwa mosatsata ndondomeko yake. Izi zikuchitika pamene mafumu atsopanowa alowa mwezi wachinayi asakulandira mswahara.

“Ndalembera unduna wa maboma a ang’ono kuti achotse mafumu amene adakweza m’dera langa. Awa ndi magulupu ndi nyakwawa zomwe zilipo 76. Adawakweza pazifukwa za ndale,” T/A Kabunduli ya m’boma la Nkhata Bay yatemetsa nkhwangwa pamwala.

Koma mkulu woyang’anira nkhani za mafumu mu unduna wa zamaboma a ang’ono, Lawrence Makonokaya wati sadalandire kalata ya Kabunduli ndipo wati mfumuyi ikatumire kalatayo kwa DC wa boma lake kuti afikitse kuundunawu.

Izi zikudza kutsatira mkwezakweza womwe Banda adachita pa zaka ziwiri zomwe wakhala akulamula dziko lino ndi chipani chake cha PP. Pa zakazi, Banda adakweza mafumu 40 000.

Ku Nkhata Bay, Kabunduli akuti mafumuwa amakwezedwa mosatsata ndondomeko zomwe zidachititsa kuti adye khonde ndi magulupu ake 14 ndikulembera undunawu kuti uchotse mafumu atsopanowa.

“Sikuti ndi mafumu onse, madera ena zidayenda bwino koma mafumu 76 ndi amene kulongwedwa kwawo kukudabwitsa,” adatero Kabunduli. “Amapatsa ufumu ena oti si mbadwa za boma lino. Ena ndi ogwira ntchito m’boma monga olondera kunkhalango, alangizi a zaulimi komanso ena ndi atsogoleri a chipani.”

Iye akuti magulupu komanso nyakwawa zakale akhala akumudandaulira za mafumu atsopanowo.

“Mafumu akalewa akaitanitsa chitukuko amadabwa kuti anthu ena sakubwera, kuwafunsa umadzidzimuka kumva kuti adapatsidwa ufumu. Mavuto ndi ambiri, kodi inuyo angakulembereni munthu wina muofesi yanu osakudziwitsani?” akudabwa Kabunduli yemwe akuti sadauzidwepo ndi boma pokweza mafumuwo.

“Izi ndi ndale. Ndidalemba kalata mu April kudandaulira boma lapitali koma sadandiyankhe. Pano ndalembanso kalata kupempha boma latsopanoli kuti lichotse mafumuwa,” adatsimikiza Kabunduli amene wati kalatayo idatumizidwa pa 27 June.

M’madera ena monga Mwanza, Thyolo ndi Machinga, mavutowa akuti sadachulukire monga zilili ku Nkhata Bay.

Mafumu a m’mabomawa akuti mavuto amene ayanga kumeneko ndi kusalandira mswahara maka kwa mafumu atsopanowa.

Senior Chief Nthache ya m’boma la Mwanza yati kumeneko mafumu onse 50 amene adakwezedwa m’dera lake akuyenda mayomayo ndipo mwezi uno ndi wachinayi.

“Mafumu akale onse akulandira bwinobwino koma atsopanowa ndiye sakupeza kanthu,” adatero Nthache.

Senior Chief Kawinga wa m’boma la Machinga akuti kumenekonso kuli mdima maka ndi mafumu atsopanowa omwe alipo 93 m’dera lake.

Koma Makonokaya akuti mafumu atsopanowa sadaikidwe pamndandanda woti ayambe kulandira ndalama chifukwa akudikirira ndondomeko ya zachuma ya 2014/15 yomwe sidaperekedwe kunyumba ya Malamulo.

Pakhala pali kukolana pakati pa mtsogoleri wa dziko ndi mafumu kaamba koti mphamvu zonse zili m’manja mwake zokweza ndi kuchotsa mfumu.

Kodi kugwebanaku kungathe bwanji?

Kadaulo pandale ndi kuonetsetsa kuti mphamvu zikupita kwa anthu, Augustine Magolowondo, akuti mavutowa azichitikabe “chifukwa mpaka pano sitidapezebe udindo weniweni wa mafumu” pamene dziko lino likutsata ndale za demokalase.

“Tili ndi lamulo lokhudza mafumu lomwe lidakhazikitsidwa mu 1967. Panthawi imene lamuloli limakhazikitsidwa, dziko lino nkuti lili pansi pa ulamuliro wa chipani chimodzi. N’chosadabwitsa kuti lamuloli limatenga mafumu ngati mbali imodzi ya boma kuiwala kuti boma limayendetsedwa ndi anthu a ndale,” watero Magolowondo.

Iye wati mavutowa akula kwambiri lero chifukwa andale amagwiritsa ntchito mafumu ngati zida zopititsira patsogolo zofuna zawo.

“Mafumu ena adyera amatengerapo mwayi wosatayana ndi andalewo kuti awaganizire. Tionetsetse udindo wa mafumu pokozanso malamulo athu ndipo mpungwepungwe wotere sudzakhalapo,” akutero Magolowondo.

Related Articles

Back to top button