Nkhani

Mai Banda wati Mafumu asalowe ndale

Listen to this article

Mafumu ena a ku Thyolo, Blantyre komanso Chiradzulu akaonekera kale kuchipani cha DPP pamodzi ndi aphungu a Nyumba ya Malamulo a ku dera kwawo ati kukawaikira aphunguwo umboni kuti anthu awo awavomereza kuti atuluke kuzipani zawo n’kulowa cha PP chomwe mtsogoleri wake ndi Pulezidenti Joyce Banda.

 

M’sabatayi, Tamvani idatsinidwa khutu kuti izi zidachitika Lachisanu sabata yatha pa 27 Epulo.

Zonsezi zikudza patangotha sabata ziwiri mtsogoleri wa dziko lino, Banda, yemwenso ndi mtsogoleri wa chipani cha PP, atauza mafumu 200 a m’zigawo zonse zitatu pa nkhumano ku hitela ya Mount Soche mu mzinda wa Blantyre kuti asalole kugwiritsidwa ntchito ndi anthu andale.

Mwazina, mtsogoleriyu adatsimikiziranso mafumuwa kuti wawakhululukira zomwe akhala akumunyoza muulamuliro wa mtsogoleri wakale, malemu Bingu wa Mutharika.

Pakhale otsutsa

Apa katswiri wa phunziro la mbiri yakale ku sukulu ya ukachenjede ya Chancellor College, Pulofesa Chijere Chirwa kudzanso mkulu wa bungwe lomenyera ufulu wa chibadwidwe la Malawi Watch, Billy Banda alosera kuti pali chiopsezo kuti dziko lino silidzikhalanso ndi zipani zotsutsa zamphamvu ngati mafumu angapitirize kugudukira ku chipani cholamula m’dzina loti akugwira ntchito ndi boma lolamula.

Awiriwa ati mafumu akuyenera kudziwa ntchito yawo chifukwa pamalamulo ngakhale pachikhalidwe mafumu sayenera kuonetsa mawanga achipani.

Chirwa wati ngati aphungu akufuna kumva maganizo a anthu akuyenera adzere kukomiti ya chipani cha m’mudzi, osati kudzera kwa mafumu chifukwa sayenera kulowerera ndale.

Apa anthu ena otumikiridwa ati ataya chikhulupiriro ndi mafumuwa komanso akana kuti adatumapo mafumu awo kuti akachitire phungu wawo umboni.

Anthuwa ati tsopano akudabwa kuti chenicheni chikuchititsa zonsezi n’chiyani.

Wotitsina khutuyo adati idali nkhumano yomwe siidalole kuti atolankhani adziwitsidwe.

“Ma T/A angapo a ku Blantyre, Chiradzulu ndi Thyolo anabwera ndi aphungu awo a chipani cha DPP.

“Aphunguwo akuti adapempha mafumuwo kuti awaperekeze kuchipani cha PP kukakumana ndi mlembi wamkulu kuti akalowe chipani cha PP n’cholinga chofuna kuthandizira mfundo zachitukuko cha boma.

“N’kutheka mafumuwa ndiwokondwa ndi Mayi Joyce Banda, ngakhale ena mwa iwo akhala akuwanyoza,” adatero wotitsina khutuyo.

Mafumu ndale ayi

Chirwa wati dziko lino likuyenera kukhala ndi mafumu okumva zomwe mtsogoleri wa dziko lino adanena kuti asagwiritsidwe ntchito ndi andale.

“Mafumu akuyenera azilimbikitsa chitukuko, chikhalidwe komanso nkhani za malo. Malinga ndi malamulo, mafumu amakhala maso a pulezidenti monga mtsogoleri wa fuko, osati wa chipani.

“Mafumu ndi eni nthaka, kotero [asazigulitse kwa pulezidenti] koma pulezidenti awatumikire, ngakhale chipani chake chikulamula.

“Kupanda kutero zingaphe demokalase chifukwa nthawi zonse akumati akuthandiza chipani cholamula,” adatero Chirwa.

Billy Banda wati m’boma la malemu Bingu wa Mutharika zinthu zidasokonekera chifukwa cha mafumuwa chifukwa samamuuza zomwe anthu kumudzi akufuna.

“M’malo mwake amasangalatsa Mutharika ponena kuti akugwira ntchito ndi boma lolamula,” adatero iye.

ye wati mafumuwa sakuyenera n’komwe kuonetsa banga lililonse lachipani PP kapena kuyamba kunyoza Mutharika.

Mlimi wa chimanga komanso amajambula zithunzi m’mudzi mwa Malika kwa T/A Mpama m’boma la Chiradzulu, Edward Chimkwita, wati n’kosayenera kuti mfumu ndi phungu athamangire kumanga mfundo zokhudza anthu pamene anthuwo sadafunsidwe.

“Ngati akufuna kupita ku chipani china akayambe afikira anthu,” adatero Chimkwita.

Mafumu athe

Alick Chikopa, yemwe amagulitsa mpunga ndipo ndi wa m’mudzi mwa Namatetule kwa T/A Kuntaja m’boma la Blantyre, wati sakuona ubwino wokhala ndi mafumu chifukwa boma lililonse amasokoneza pomanama kuti akugwira ntchito ndi boma.

Iye wati aliyense yemwe ali kuderalo ali ndi maganizo ake kotero lingakhale bodza kuti anthu avomereza za ganizolo.

Mphunzitsi pasukulu ina ya pulaimale m’mudzi mwa Sambani kwa T/A Mulolo m’boma la Nsanje, Aubrey Jeke, wati phungu wawo kumeneko adali ndi msonkhano ndi magavanala akuderalo pomwe amawadziwitsa ganizo lake kuti akufuna alowe chipani cha PP.

“Akambirana koma ife sadatidziwitse ndipo sitikudziwanso kuti agwirizana chani.

“Koma ife tikufuna tidziwe bwino za ganizo lawo ndipo tipereke maganizo athu chifukwa ndife tidamuika pampando,” adatero Jeke.

M’sabatayi, wachiwiri kwa mneneri wa chipani cha PP, Kennedy Msonda, adati amayenera afunse akuluakulu ake komanso kutolera bwino zina ndi zina asalankhulepo pa nkhaniyi.

Related Articles

Back to top button