Makhoti ayambanso kugwira ntchito

Sitalaka yomwe ogwira ntchito m’makhoti amachita yatha Lachinayi.

Mtsogoleri wa ogwira ntchitowa, Charles Lizigeni, adatsimikizira Tamvani kuti makhoti onse a m’dziko muno ayambanso kugwira ntchito.

“Tagwirizana zobwerera kuntchito kaamba koti Amalawi amavutika kuti apeze chilungamo chifukwa cha sitalakayi,” adatero Lizigeni.

Ogwira ntchito m’makhoti atenga masabata anayi akunyanyaka ntchito pofuna kukakamiza boma kuti liziwapatsa ndalama zolipirira nyumba ngati momwe likuchitira ndi majaji ndi mamajisitiliti.

Koma nduna ya zachuma, Goodall Gondwe, idali yodabwa kuti majaji ndi mamajisitiliti akulandirira padera ndalama zolipirira nyumba.

“Boma lidasintha ndondomeko zolipirira ogwira ntchito ake mu 2014 moti munthu aliyense sakuyenera kulandirira padera ndalama za nyumba.

“Malipiro omwe ogwira ntchito ntchito m’boma amalandira [clean wage] adaphatikizamo kale malipiro apamwezi a munthu ndi ndalama zolipirira nyumba.

“Ngati majaji ndi mamajisitiliti akulandirira padera ndalama za nyumba ndiye kuti boma lidangolakwitsa,” idatero ndunayo.

Boma, kudzera mwa mlembi wa zachuma Ben Botolo, lidadzudzula ogwira ntchitowa ndipo lidawauza kuti sitalaka yawo siyovomerezeka ndi malamulo a dziko lino. Boma lidauza anthuwo kuti abwerere ku ntchito.

Botolo adati n’zosatheka kuti boma liziwapatsa ndalama za nyumba zoyambira m’chaka cha 2012.

Koma Lizigeni adatsutsa zomwe mlembiyu adalankhula. “Sitalaka yathu ndi yovomerezeka. Ngakhale tikubwerera kuntchito sizikutanthauza kuti sitalaka yathu idali yosavomerezeka.”

Anthuwa adayenera kuyamba ntchito Lachitatu, koma adakana kutero ndipo adapempha kuti apolisi omwe adadzadza m’makhoti achokeko kaye.

Sitalakayi idayamba pa July 31 m’makhoti onse a m’dziko lino.

Share This Post