Nkhani

Makuponi otsiriza afika m’zigawo

Mabanja ovutikitsitsa tsopano akhoza kumwetulira kutsatira kaamba ka kubwera kwa makuponi otsiriza a zipangizo zaulimi zotsika mtengo.

Boma lati lalandira makuponi omaliza, zomwe zipangitse kuti alimi ovutikitsitsa 812 100 apeze zipangizozi m’zigawo za pakati ndi kumpoto.fisp

Makuponiwa abwera panthawi yomwe aphungu a ku Nyumba ya Malamulo komanso atsogoleri a mabungwe omwe si aboma akhala akudzudzula boma chifukwa cha kuchedwetsa pogawa makuponi komanso ganizo loyamba kugawa makuponi m’chigawo cha kummwera.

Wachiwiri kwa mkulu woyendetsa ndondomeko ya zipangizo za ulimi zotsika mtengo muunduna wa zamalimidwe, Osborne Tsoka, adatsimikiza za kufika kwa makuponiwa ndipo adaonjezera kuti boma lamaliza kusankha anthu omwe alandire makuponiwa m’maboma 27 ndipo boma la Dowa lokha ndiko ntchitoyi ikupitirira.

Tsoka adafotokoza: “Tikudziwa kuti tikuthamangitsana ndi nthawi. Ichi ndi chifukwa chake tamwanza anthu kuti akhale  akupereka makuponiwa kwa alimi m’zigawo ziwiri zomwe zinali zisanalandire. Padakalipano, makuponi anyamulidwa kupita m’maboma omwe anthu adali asanalandire.

“Tikakamba za maboma, boma la Dowa ndilo latsala kuti timalize ntchito yosankha anthu omwe alandire makuponiwa. Ndikukhulupirira kuti pofika kumapeto a sabatayi ntchitoyi ikhala itatha.”

Poyankhula mwapadera, nduna ya zaulimi ndi chitukuko cha madzi Dr Allan Chiyembekeza adati sadatekeseke ndi chikayiko cha mabungwe omwe si aboma chakuti ndondomekoyi chaka chino ikumana ndi zokhoma.

Sabata yatha, boma lidalandira makuponi oyamba ofikira anthu 687 900 m’chigawo cha kumwera.

Koma potsirapo ndemanga pa anthu ovitikitsitsa omwe alandire makuponiwa chaka chino, mafumu ena, maka m’chigawo cha kumpoto adandaula kuti kusankha maina sikunayende bwino chaka chino chifukwa ena omwe asankhidwa kuti alandire nawo si anthu ovutikitsitsa, koma opeza bwino chifukwa ali m’zintchito zolipidwa pamwezi.

Ku Rumphi, nyakwawa ina ya m’dera la Gulupu Chikulamasinda kwa Themba la Mathemba (Paramount Chief) Chikulamayembe, idati ndi yokhumudwa chifukwa mwa anthu 9 omwe alandire makuponiwa m’mudzi mwake asanu ndi oti sali pamudzipo koma m’zintchito monga ku Blantyre, ku Lilongwe ndi ku Mzuzu komanso wina ndi mphunzitsi ku Kasungu.

“Inde ndi a m’mudzi mwanga, koma si ovutikitsita. Ine mwini wakene ndimagwira ntchito ku Blantyre koma dzina langa latuluka pamndandanda wa omwe apindule ndi makuponiwa kusiya anthu ovutikitsitsa m’mudzi mwanga.

“Sindidziwa kuti amasankha bwanji mainawa chifukwa akadatifunsa mafumufe kuti woyenera ndani kulandira makuponi tikadawapatsa maina a anthuwo, osati kusankha okha. Okhala ndi anthu ndan, iwowo kapena ife mafumu?” idafunsa mfumuyo, yomwe sidafune kuti itchulidwe poopera mawa.

Mafumu ena monga Gulupu Mtanthira ndi ena kwa Chikulamayembe adavomereza pocheza ndi Tamvani kuti kasankhidwe ka maina chaka chino sikadayende bwino. n

Related Articles

Back to top button