Malawi ali pamoto—Kapito

Mkulu wa bungwe loona ufulu wa ogula la Consumers Association of Malawi (Cama), John Kapito wati boma likuyenera kutulutsa chimanga chomwe chikusungidwa m’khokwe zake kuti anthu ayambe kugula chimangachi pa mtengo wotchipa ku Admarc.

Kapito walankhula izi m’sabatayi potsatira ganizo la bungwe la Admarc lokweza mtengo wa chimangachi.

Pa 21 Disembala, bungweli lidakweza mtengo wa chimanga.

Thumba lolemera makilogalamu 50 lidayamba kugulitsidwa pa K3 000 kuchoka pa K2 000.

Apa Kapito waunikira kuti uku ndikupha kapena kulanga Amalawi pomwe asadalakawe.

Iye wati chimanga chomwe bungwe la Admarc likukweza ndichomwe lidagula lokha kutsatira kulephera kwa boma kupereka ndalama ku bungweli.

“Nkhaniyi ndiyovutirapo chifukwa choti chimanga chidasamutsidwa kuchoka ku Admarc kupita ku boma.

“Chimanga chomwe chimasungidwa ndi Admarc sichaboma. Chimanga cha boma chimakhala kunkhokwe zaboma, ndiye aboma ndiwo amauza a Admarc kuti awagulitsire.

“Chimangachi Admarc idagula yokha ndi ndalama zawo kuchokera ku banki chifukwa choti boma lidakana kuwapatsa ndalama.

“Tisayang’ane Admarc, koma tiyang’ane boma kuti litulutse chimanga chimene chilipo munkhokwe; pajatu boma limati amanga nkhokwe momwe muli chimanga chambiri,” adatero Kapito.

Iye adati izi zikachitika, kumsika wa Admarc kukhala chimanga chotsika mtengo.

Kapito wati vuto lina n’kuti boma lidagulitsa chimanga kunja, zomwe zachititsa kuti chimanga chiyambe kusowa m’dziko muno.

Mavenda nawo akwezanso mitengo.

Ku Mbayani mumzinda wa Blantyre, thumba la chimangali lili pa K3 500 kutsatira kukweza kwa a Admarc.

Lawrence Mizati wa m’mudzi mwa Chimbeta kwa T/A Changata m’boma la Thyolo wati kukweraku kukhudza anthu ambiri chifukwa kwadza nthawi yomwe mavuto m’dziko muno ali posasimbika.

Caroline Malemia wa m’mudzi mwa Mdala kwa T/A Machinjiri m’boma la Blantyre wati kudera lawo chimangachi chakwera kwambiri, maka mwa mavenda, zomwe zikuika moyo wawo pachiopsezo.

“Kilogalamu ya chimanga ili pa K80 kuchoka pa K55; thumba lili pa K4 000. N’kovuta kuti omwe ali ndi mabanja akulu akwanitse kugula.

“Zinthu sizili bwino kotero boma likuyenera kuganizira omwe tikuvutika,” adatero Malemia.

Share This Post