Nkhani

Malawi sisewera ndi Uganda

Listen to this article

Chiyembekezo chidalipo kuti Malawi iswana ndi Uganda kuti ikonzekere masewero a World Cup  pa 7 October pamene ikunthane ndi Tanzania.

Koma mlembi wa bungwe loyendetsa masewero m’dziko muno la FAM, Suzgo Nyirenda, walengeza kuti izi sizithekanso chifukwa osewera a Flames amene amasewera mpira wawo kunja kwa dziko lino sakwanitsa kudzasewera masewerowo chifukwa makalabu awo akhala otangwanika.Flames-warm-up

Malinga ndi Nyirenda, Flames idzanyamuka m’dziko muno ulendo ku Tanzania pa 4 October osachita zokonzekera ndi timu iliyonse.

Koma kochi wa timuyi, Ernest Mtawali, pofuna kupima mphamvu za anyamata ake, adakonza masewero ndi FISD Wizards Lachitatu ndipo Flames idapambana 4-0.

Flames idzakumananso ndi Tanzania pamasewero achibwereza pa 11 October pa Kamuzu Stadium mumzinda wa Blantyre.

Related Articles

Back to top button