ChichewaEditors Pick

Manja m’khosi ndi kupsa kwa misika

 

Pamene nkhani yakupsa kwa misika yayala nthenje m’dziko muno, amalonda ena achita jenkha, kusowa mtengo wogwira katundu wawo atasakazidwa ndi moto.

Posakhalitsapa, misika ya Area 18 ku Lilongwe, wa Kasungu, Vigwagwa ku Mzuzu, Kamuzu Road ku Salima komanso wa Karonga yapsa ndipo katundu wa nkhaninkhani wasakazidwa.

Mmodzi mwa okhudzidwa ndi kuyaka kwa msika wa Vigwagwa wati akusowa mtengo wogwira pamene katundu wake wa K1.3 miliyoni adayakiratu.

Kupsa kwa misika ndiyo nkhani ili mkamwamkamwa
Kupsa kwa misika ndiyo nkhani ili mkamwamkamwa

“Ndithandiza bwanji abale anga 11 omwe amadalira ine? Chopweteka kwambiri nchakuti ndidali nditangotenga ndalama kumene kukagula katunduyo,” adatero Banda.

Wapampando wa komiti ya pamsika wa Vigwagwa, Gerald Maulana, adati komiti yoona za ngozi za moto yapangidwa yomwe iziona za momwe angathanirane ndi ngozizo komanso kupezeka kwa madzi ozimitsira moto azikhala pafupi.

Maulana adati anthu omwe adali ndi ngongole akuwathandiza powalembera makalata opita kukhonsolo ndi mabungwe opereka ngongole ngati umboni kuti katundu wawo adapsa.

Iye adati: “Zaka za m’mbuyozo anthu ankagwiritsa ntchito moto ngati njira yobela katundu koma apolisi adakhwimitsa chitetezo ndipo palibe amene adadandaula kubedwa kwa katundu pa nthawi ya moto.”

Ndipo Lachitatu polankhula phungu wa pakati m’boma la Kasungu Amon Nkhata atapereka simenti yokwana K1.5 miliyoni yogulira matumba 200 a simenti kuti msika wa Kasungu umangidwenso, wapampando wa mavenda mumsikawo Burnet Saudi adati padakalipano manja awo ali m’khosi.

“Tikupempha akufuna kwabwino ena athandize m’njira zosiyanasiyana chifukwa mavuto ndiye ngambiri,” adatero iye.

Padakalipano, mneneri wapolisi m’dziko muno Rhoda Manjolo wati apolisi amayamba afufuza kaye asanamange munthu. Mawuwa adadza pamene mneneri wa unduna wa maboma aang’ono Muhlabase Mughogho adati kusamangidwa kwa anthu ootcha misika ndiko kukuchititsa mchitidwewu kuti ukule.

Mughogho adati palibe chasintha pa mfundo za chikalata chimene undunawo udatulutsa chaka chatha.

Malinga ndi chikalata cha chaka chathacho, makhonsolo ayenera kukhala ndi zozimira moto zokwanira m’misika kuti ngozi itagwa asasowe mtengo wogwira.

“Malo ogulitsira akuyenera kukhala omangidwa ndi njerwa. Misika isamakhale malo othinana kwambiri. Komanso misika iyenera kutetezedwa ndi inshuransi kuti ngati ngozi yamoto igwa,” chidatero chikalatacho. n

Related Articles

Back to top button