Chichewa

Mantha pa Wenela

Listen to this article

Titakhala pamalo aja timakonda pa Wenela, adafika gogo wina. Iye adavala nkhope yachisoni.

“Ana inu, mwataya chikhalidwe. Mwalowerera kuba, kupha ndi kuononga. Inu, a satana oyenda ndi mapazi,” adatero gogo uja.

Tonse tidadabwa kuti nkhaniyo imayambiranso pati.

“Bwanjinso, gogo? Chavutanso n’chiyani?” adafunsa Abiti Patuma.

art

“Ndinu alendo kodi pano pa Wenela kuti simunamve za kuphedwa kwachitika masiku apitawa? Wophedwayotu adakaponyedwa pafupi ndi nyumba ija munkakhala Mfumu Mose,” adafotokoza gogoyo.

Abale anzanga, pa Wenela paterera. Kukacha, nkhani za kuba mbweee! Kuphana ndiye kudya kwa awa ndi awo.

“Palibetu chimene chikuyenda. Mwinatu tingolimbikira ufiti chifukwa njala nayo ndi iyi ili pakhomopo,” adatero gogo uja.

“Chaka chinonso galu wakuda adutsa? Abale tidyenso mapira, mchewere ndi nyika?” adafunsa Abiti Patuma.

“Anthu ayamba kale kudya zimenezo. Simunalowere ku Nsanje pakatipa?” ndidafunsa.

Apa Gervazzio adaika nyimbo ina yake:

Lili kuti lili kuti mnzanga dziko lija

Lomwe ana ankangothawa

Kuthawa njoka osati munthu….

“Masiku amakedzana, makwangwala akuikira pansi, kudalibe kuphana umu mukuchitira leromu. Kodi mwalowa chiwanda chotani m’mitima mwanumo? Inde mudzithemba u-mafia koma dziwani nthawi imakwana,” adatero gogo uja.

Chifukwa chokoledwa ndi nkhani zachisoni zidayala nthenje pa Wenela, Abiti Patuma adati tilowere ku sitediyamu, chifukwa kudali mpira. Ndidavomera monyinyirika chifukwatu kubwalo la masewera limeneli tsopano kwalowa mphepo ina. Mukukumbukira wina adafako miyezi yapitayo. Mwakumbukanso ena adavulala tsiku lokumbukira kuti pa Wenela timadzilamulira tokha ife ojiya, osenza ndi osolola, sitilabada za British Overseas Main Administration imene idamanga goli tate, mayi ndi ana awo.

Mukumbukatu bwino tsiku lija Moya Pete adathawa anzake awiri ati kukafuna kuchezetsa abale ena m’tauni.

“Zidali ngati kholo loitana mnzake kuchisangalalo chakuti mwana wake wakwanitsa zaka 51. Mnzakeyo atabwera pakhomopo, tate wa mwanayo nkumamutsanzika kuti akupita m’tauni ndipo mlendo akhoza kumaonera kanema,” adatiuza Abiti Patuma.

“Musamutero Moya Pete. Ndikumvatu kuti adachoka mpira uli mkati chifukwa anali atatopa zedi. Komansotu paja akuti amakonda kugona osati masewero,” adatero Gervazzio.

“N’chifukwa chaketu ndimaona ngati ndi bwino akadati munthu wotenga mpando wa Mfumu Mose asamadutse zaka 60. Lero taonani mkulu wa zaka 90 akuyang’anira anyamata othamanga magazi a zaka zosaposa 60 amene akhoza kumupusitsa kuti achoke pakhomo patafika alendo,” adatero gogo uja.

“Zoona adamuuza kuti sakhala woyamba chifukwa gogo uja adapeza Tadeyo asanavale zovala kwawo kwa Kanduku naye sankamaliza kuonera mpira wadolola,” adatero Abiti Patuma.

Titafika kubwalo la masewero, tidalandiridwa ndi utsi wokhetsa misozi.

“Koma masewero tadana nawo chiyani. Onani apolisi awo akuombera uyo, uyo, uyo! Tikabisala kuti?” ndidalira.

Abale anzanga, tivomereze kuti pano pa Wenela zinthu zatilaka. Mwina tilimbikire ufiti, uthakati basi.

Gwira bango, upita ndi madzi!!

 

Related Articles

Back to top button
Translate »