Nkhani

 Maphunziro a chidyerano cha chimbudzi athandiza

Moyo wasintha ndipo kamphepo kayaziyazi kakudutsa tsopano m’midzi 13 yozungulira dera la T/A Njewa ku Lilongwe anthu atasintha khalidwe lochitira chimbudzi paliponse nkuyamba kugwiritsa ntchito zimbudzi.

Zaka 51 chilandirireni ufulu odzilamulira, anthu kuderali amadalirabe tchire ndi kuseli kwa mitengo akafuna kudzithandiza kufikira pomwe bungwe la Plan International lidawafikira ndi maphunziro akuipa kochitira chimbudzi paliponse.Modern-toilets-at-Tawuka-School-(1)

Bungweli lidaphunzitsa anthuwa kuti akamachitira chimbudzi paliponse ndiye kuti akuchita chidyerano cha zopambukazo pakati pa wina ndi mnzake zomwe zingawabweretsere matenda otsegula mmimba ndi mmapapo kaamba kafungo loipa.

Njewa adatsimikiza kuti kwanthawi yaitali anthu m’dera lake samadziwa kufunika kwa chimbudzi ndipo mmimba mukafunda amangolowa patchire nkukadzithandiza ndipo adati pachifukwachi, m’derali mumabuka matenda osiyanasiyana pafupipafupi.

“Padalibe zoti wamkulu kapena mwana ayi. Aliyense amati akamva m’mimba, kokapumira kudali kutchire ndiye padalibe zaulemu chifukwa nthawi zina mwana amatha kupezerera wamkulu akudzipeputsa komanso matenda samati abwera liti,” adatero Njewa.

Iye adati nthawi zina alendo amadziwira fungo kuti afika m’dera la Njewa chifukwa chimbudzi chidali ponseponse mpaka liti,” adatero Njewa.

Iye adati nthawi zina alendo amadziwira fungo kuti afika m’dera la Njewa chifukwa chimbudzi chidali ponseponse mpaka anthu kumachita nkhawa poyenda m’tchire kuopa kuponda chimbudzi cha munthu wina. choyamba adafotokozera anthuwo kuti amadyerana chimbudzi pazomwe amachitazo.

Mlongoti adafotokoza kuti zidawatengera miyezi iwiri kuti anthu amvetsetse momwe amadyera chimbudzi cha anzawocho ndipo atamvetsetsa

adayamba kukumba zimbudzi zomwe akugwiritsa ntchito pano.

“Lidali dera lomvetsa chisoni kwambiri pankhani yaukhondo. Poona kuti tivutika kumvana nawo msanga, tidagwiritsa ntchito chionetsero.

Tidatenga chimbudzi chachiwisi nkukhazika apo kenako nkuyika nsomba pa makala ndiye okha amaona kuti ntchentche zimatera pachimbudzi chija nkukateranso pa nsomba mpomwe adamvetsetsa za chidyerano cha chimbudzi,” adatero

 

Woyang’anira ntchito zotukula midzi kubungwe la Plan International, Chimwemwe Mlongoti, adati iwo atafika mderari

Related Articles

Back to top button