Nkhani

Maphunziro alowa nthenya

Listen to this article

…Okhudzidwa ndi ngozi akuphuphabe

Nthawi ili cha m’ma hafu pasiti leveni (11:30 am) ndipo kunja kukutentha koopsa. Ena mwa ophunzira pasukulu ya pulaimale ya Chikoja kwa mfumu Osiyana M’boma la Nsanje akuphunzirira pansi pamtengo wopanda masamba, ena ali m’matenti momwe mukutentha molapitsa. Ofesi ya aphunzitsi ili pansi pamtengonso umene masamba ake adayoyoka.

Class under a tree: A sign of Malawi’s failure in education

Posakhalitsa wophunzira wa Sitandade 4 wakomoka chifukwa chotentha ndipo ophunzira anzake akudzithira madzi kumutu pofuna kuziziritsa matupi awo.

Awa ndiwo mavuto amene amanga nthenje pasukulu ya Chikojayi, yomwe idakhudzidwa ndi madzi osefukira.

Nazonso sukulu za Chingoli m’boma la Mulanje ndi Mvunguti m’boma la Phalombe akukumana ndi zokhoma zokhazokhazi.

Pamene patha miyezi 8 chichitikireni ngoziyi, nyumba za aphunzitsi, zimbudzi komanso mabuloko ndi maofesi a aphunzitsi sizidakonzedwe, zomwe zikupereka mantha kuti mavutowa angakhodzokere mvula ikayamba mwezi ukubwerawu malinga ndi azanyengo.

Wachiwiri kwa mphunzitsi wamkulu pasukulu ya Chikoja, Clement Seda, akuti ngati mvula itayambe ndiye zivutitsitsa. “Panopa tikupirira dzuwa, koma ngati mvula ikayamba ndiye palibe chabwino, sukulu idzatsekedwa kaye.”

M’boma la Nsanje, madzi osefukira adagwetsa sukulu ya Chinama ndi Namiyala. Izi zidachititsa kuti boma limange matenti kuphiri la kwa Osiyana kwa T/A Mlolo kuti ophunzira azikaphunzirirako pamene matenti ena adamangidwa kwa Chambuluka.

Kumangidwa kwa matentiwa, chidali chimwemwe kwa aliyense kuti basi athana ndi mavuto osefukira kwa madzi, koma lero kwaipa pamene mavuto ena afika m’khosi.

Seda akuti boma lidalonjeza kuti ayamba kuwamangira sukulu nthawi ya mvula isadayambe. Koma mpaka lero kuli chuu.

“Adatimangira matenti asanu ndipo makalasi ena akuphunzirira panja. Poyamba tinkadandaula ndi ana amene ankaphunzira panja, koma pano tikudandaulanso ndi matentiwa chifukwa mukutentha kwambiri. Mwaona nokha kuti mwana wina kuti Sali bwino, mavuto amenewa achulukira chifukwa matenda amutu si nkhani,” adatero Seda.

Seda adati aphunzitsi onse akukhala ku Fatima ndi Makhanga, womwe ndi mtunda wa makilomita osachepera 14.

“Tikafulumira kufika kuntchito ndiye kuti ndi 8:30 mmawa kusonyeza kuti piriyodi imodzi imadutsa tisanafike, komanso chifukwa chotentha, ophunzira amaweruka mofulumira dzuwa lisadafike powawitsa.

“Izi zikuchititsa kuti ana asaphunzire mokwanira, komanso ambiri sakubwera chifukwa cha mavuto amene tikukumana nawowa,” adatero Seda.

Iye adati izi zachititsa kuti zotsatira za mayeso a Sitandede 8 chaka chino zikhale zosokonekera. Mwa ana 40 amene adalemba mayeso a PSLC, ana 4 okha ndiwo adakhoza pomwe chaka chatha ana ana onse 35 adakhoza.

“Mu 2013 adalemba ana 85 ndipo onse adakhoza, mu 2012 ana 29 adalemba mayeso ndipo 27 ndiwo adakhodza. Sukuluyi yakhala ikuchita bwino kuyambira mmbuyo monse,” adatero Seda, amene sukulu yake ili ndi ophunzira 900.

Koma mneneri muunduna wa zamaphunziro Manfred Ndovi adati timupatse nthawi kuti afotokozepo zomwe boma likuchita kuti lipulumutse ophunzirawa.

Nayo sukulu ya Chingoli pulaimale m’boma la Mulanje akuti mavuto ndi ankhaninkhani malinga ndi DC wa m’bomalo Fred Movete.

“Chimangireni matenti palibe chimene chachitikapo, mabuloko sadayambe kumangidwa moti zivuta kwambiri mvula ikayamba koma ndangomva kuti mapulani alipo kuti mabuloko amangidwa,” adatero Movete.

DC wa boma la Phalombe Paul Kalilombe akuti m’bomalo mavutowa ndi ochepa kuyerekeza ndi maboma ena.

“Sukulu ya Mvunguti ndiyo idakhudzidwa, makalasi awiri okha ndiwo akuphunzira m’matenti koma ena ali m’mabuloko,” adatero Kalilombe.

Maboma 15 ndiwo adakhudzidwa ndi ngozi ya madzi mu January chaka chino koma boma la Mulanje, Nsanje ndi Phalombe ndi omwe sukulu zidakhudzidwa.

Kupatula mbali ya sukulu, boma la Nsanje lakhudzidwanso ndi kusowa kwa chipatala komanso njala yomwe idagwa chifukwa chokokoloka kwa minda.n

Related Articles

Back to top button
Translate »