Nkhani

Matimu 15 mu ligi ya TNM?

Listen to this article

Chaka cha 2014 chapita ndi zochitika zake ndipo talowa mu 2015 amene tikufuna tione zina. Mbali imodzi imene tikufuna isinthe ndi ya matimu amene akusewera muligi ya TNM.

Ligiyi ili ndi matimu 15. Zikusonyeza kuti Sulom ikakonza momwe matimu asewerere, timu imodzi imakhala ikupuma.

Nthawi yomwe timu ya Big Bullets yalowa CAF, munthu wina wakunja adatifunsa kuti ndi matimu angati amene amasewera muligi yaikulu kuno?

Titayankha kuti ndi 15, iye adati: “This is madness, how do 15 teams play?” (Iyi ndiye misala, matimu 15 amasewera bwanji?) Iye sadamvetse ndipo adapitiriza: “Are you serious a big league like that one has 15 teams?” (Mukunena zoona ligi yaikulu ngati iyi ili ndi matimu 15?)

Adatipatsa zifukwa zake zomwe amadabwira.

“Tikagawa matimu momwe asewerere, sipafunika kuti timu ina izingokhala. Si bwino kuti timu ina isewere magemu awiri pamene timu ina yasewera imodzi. Komanso ndi kulakwitsa kuti timu imodzi isewere lero ndiye mawa ikasewere ndi timu yomwe dzulo sidasewere.

“Osewera amakhala atopa pamene ena avulala, akuyenera akhale ndi nthawi yopuma. Ndiye otopa angasewere bwanji ndi timu yomwe sidasewere? Kodi angapambane?”

Adatero munthuyo, uko akupempha kuti zikonzedwe kuti tikhale ndi matimu 14 kapena 16 muligiyi kuti timu iliyonse izisewera mofanana.

Pamene talowa chaka china, tikhulupirira kuti zikonzedwa chifukwa ngati zikhalabe chomwechi, kudandaula kwa matimu kuti apatsidwa magemu ambiri kusiyana ndi anzawo sikudzatha.

Related Articles

Back to top button
Translate »