Nkhani

Mavenda achita zipolowe ku Lilongwe

Listen to this article

Zinthu zidafika povuta pamchombo wa dziko lino Lachitatu ochita malonda mumsika waukulu wa mu mzinda wa Lilongwe ataletsa munthu aliyense ochita malonda mumzindawu kugulitsa katundu.

Zidafika povuta zedi mpaka mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika adakauza mavenda amachita ziwawazo kuti adekhe. Iye adati boma lichitapo kanthu choncho mavendawo asachite phuma.

Khamu la mavenda lidazungulira m’misewu ya mumzindawu kuonetsetsa kuti palibe yemwe akuchita malonda amtundu uliwonse pokwiya ndi moto olusa omwe udaononga katundu wambiri mumsikawo.

Iwo adanenetsa kuti salola munthu aliyense kuchita malonda kufikira iwo atalandira chipepeso pa katundu yemwe adaonongekayo chifukwa sadakhutire ndi chomwe chidayambitsa motowo.

“Sitilola kuti munthu wina aliyense azichita malonda pomwe ife tikungokhala chifukwa katundu wathu wapsa ndi moto omwe chiyambi chake sichikudziwika bwinobwino. Malonda apitirira pokhapokha katundu wathu atabwerera,” adatero mmodzi mwa mavenda odandaulawo.

Zinthu zidafika poopsa kwambiri pomwe mavendawa amayenda kuchoka kumsika wa kumunsi nkumalowera kumtunda komwe kuli sitolo zikuluzikulu monga Game Stores, Shoprite ndi mabanki akuluakulu uku akuimba nyimbo zosonyeza kuipidawa.

Mkulu wa mavenda a mumsika wa Lilongwe James Soko adatsutsa kuti anthu omwe amatseketsa ma sitolozo adali mavenda.

Iye adati ngozi ya motowo itachitika, mavenda adakumana nkukambirana zochita ndipo adagwirizana kuti akambirane ndi akuluakulu mwa bata koma kenako adadabwa kuona anthu akuyenda m’misewu nkumatseketsa sitolo.

Mneneri wa polisi m’dziko muno Rhoda Manjolo adati apolisi adakhwimitsa chitetezo mumzindawu pofuna kuteteza mabizinesi ataona kuti anthu ena adali ndi maganizo olakwika.

Iye adati apolisi adathamanga kukateteza katundu yemwe adapulumuka pangoziyo ndipo izi zidakwiyitsa anthu ena omwe adayamba zaupanduzo.

Moto olusawo udabuka mu msika waukulu wa mu mzindawu mma 11 koloko usiku wa lachiwiri ndipo a nthambi yozimitsa moto mothandizana ndi a sirikali a boma adalimbana ndi motowo mpaka udazima koma nkuti katundu wambiri ataonongeka.

Related Articles

Back to top button