Mavuto a ambulasi anyanya m’zipatala - The Nation Online

Mavuto a ambulasi anyanya m’zipatala

Ndi Lachiwiri m’mawa. Tili pafupi ndi nyumba yachisoni pachipatala cha Gulupu mu mzinda wa Blantyre. Rose Kaphesi, mwana wake ndi achibale atambalala padzuwa. Maso ali kunjira kudikira ambulasi.

Sabata yatha chitulukireni m’chipatala, koma ambulasi yoti iwatengere kumudzi kwawo ku Nsanje palibe.

“Sindikudziwa kuti ambulasi ibwera liti. Timayenera tinyamuke Lamulungu koma mpaka lero,” adatero Kaphesi.

Awa ndiye mavuto omwe ayanga m’zipatala za boma m’dziko muno zomwe zakhumudwitsa mkulu wa bungwe lopititsa patsogolo ntchito zaumoyo la Malawi Health Equity Network (Mhen), George Jobe.

Tamvani yapezanso kuti amayi 15 adaberekera panjira chaka chino chokha pachipatala chaching’ono cha Kandeu m’boma la Ntcheu pamene amapita kuchipatala cha boma cha Ntcheu kuti akathandizidwe.

M’modzi mwa ogwira ntchito pachipatalapo, amene sadafune kutchulidwa, adati vuto lakusowa kwa ambulasi lafika powawa.

“Tidauzidwa kuti tilandira ambulasi mu 2009, adati timange malo wosungira ambulasiyo koma mpaka pano kuli chuu!” iye adatero.

Kandeu ili pamtunda wa makilomita 36 kukafika kuchipatala chaboma. Anthu akuti amatengedwa pa machila kapena panjinga popita kuchipatala chachikulu.

“Nthawi zina amatengedwa pa matola ndipo amalipira K20 000 kuti akawasiye kuchipatala,” adaonjeza wachipatalayu. “Chaka chino chokha anthu 15 aberekera panjira ndipo m’modzi adamwalira m’njira.”

Nako kuchipatala cha Chilipa m’boma la Mangochi akuti anthu awiri amwalira chaka chino pamene amadikirira ambulasi kuti idzawatenge.

Wapampando wa chipatala cha Chilipa, nyakwawa Nkaya ya m’dera la T/A Chilipa, yati ali ndi ambulasi imodzi yokha yomwe ikutumikira zipatala zisanu.

“Tili ndi chipatala cha Chilipa, Katema, Mtimabi, Phirilongwe ndi Kapire komwe ikutumikira. Ndi mitunda yotalikirana ndi makilomita 40 komanso misewu yake siyabwino,” idatero mfumuyi.

Iye wati wakhala akudandaula koma yankho palibe. “Kuti ambulasi ichokere ku Mtimabi kudzafika ku Chilipa, ndi nthawi yaitali. Izi ndizomwe zidachititsa kuti anthu awiri amwalire amene amafunika atumizidwe kuchipatala cha Mangochi,” adatero Nkaya.

Pachipatala cha Masasa ku Dedza ndi Balaka odwala amawauza kuti agule mafuta kuti ambulasi iwatumikire.

Pachipatala chaboma cha Rumphi, mavuto akulanso malinga ndi mneneri wachipatalachi Bwanalori Mwamlima.

“Tidali ndi ambulasi 6, pano 4 sizikuyenda. Mavuto alipo kuti tikafike ku Hewe komwe ndi mtunda wa makilomota 60,” adatero Mwamlima.

Chipatala cha Nkhotakota pali ambulasi imodzi yokha. Mkulu pachipatalachi Jimmy Phiri wati kusayenda kwa ambulasi zina kwadzetsa mavuto akulu.

Koma Jobe akuganiza kuti unduna wa zaumoyo udakapatsidwa ndalama zambiri mavutowa akadachepa.

“Tili ndi mavuto ambiri m’zipatala amene akufunika ndalama zambiri. Pali mavuto azakudya komanso mayendedwe. Mavutowa kuti athe pakufunika ndalama zambiri.

“Maboma ena ali ndi ambulasi koma akulephera kukonzetsa. Ena vuto ndi kuchepa kwa madalaivala. Nthawi zina vuto ndi mafuta womwe akuchititsa kuti wodwala azisonkha ndalama kuti ambulasi iyende. Izi n’zachisoni ndipo boma lichitepo kanthu msanga,” adaonjeza Jobe.

Mmodzi mwa akuluakulu aku unduna wa zaumoyo Beston Chisamile wati boma lili ndi mapulani ogula ambulasi zina.

“Mavuto alipo koma tili ndi mapulani oti tigule ambulasi zina,” adatero Chisamile.

Share This Post