Chichewa

Mayi wamalonda avulazidwa ku bt

Listen to this article

Titha Masamba, wa zaka 31, akumva ululu wadzaoneni. Kuti ayende akuyenera agwirire ndodo; sangagone chafufumimba koma chammbali kapena chagada; moyo wamtendere watha.

Akuti adamuphera tsogolo lake: Masamba kumva ululu kunyumba kwake
Akuti adamuphera tsogolo lake: Masamba kumva ululu kunyumba kwake

Akuti izitu zili chonchi chifukwa cha bala lomwe lili pabondo lake la kumanja lomwe lidasokedwa kuchipatala pambuyo pokhapidwa ndi chikwanje.

Ulendo wa mayiyu wokagulitsa mandasi pa 7 July ndi womwe udabweretsa mavutowa pomwe anthu ena, omwe akuwaganizira kuti ogwira ntchito kukhonsolo ya mzinda wa Blantyre (city rangers) amene adamuchita chiwembu pomulanda malonda ake komanso kumuvulaza ndi chikwanje.

Masamba akuti atangomwalira amuna ake mu 2007, iye adayamba geni yogulitsa mandasi kuti azisamalira banja lake la ana awiri. Malo amene amagulitsira malonda akewo akuti ndi ku Cold Storage pafupi ndi Kamuzu Stadium mumzindawu.

Monga mwa nthawi zonse, patsiku la ngozilo, adauyatsa ulendo wokapha makwacha. “Pafupi ndi Cold Storage pali njanje ndiye ndidaika malonda anga chapafupi ndi msewu womwe umadutsa pamwamba pa njajeyo kuti ndikataye madzi ndisadalowere ku Cold Storage,” adatero Masamba.

“Pamene ndimati ndikatenge malondawo, ndidangoona galimoto ya City, yoyera ndipo mmbalimu idali ya sefa. Idadzaima pafupi ndi pomwe padali mandasiwo ndipo adali m’galimotomo adatsika natenga beseni la mandasilo. Ena adandigwira ndipo ndidawauza kuti angotenga mandasiwo asalimbane nane koma zidakanika.”

Mayiyu, yemwe akukhala ku Makhetha mumzindawu, akuti anthuwo adamubudulira malondawo ndipo mosakhalitsa zodabwitsa zidamuchitikira.

“Mmodzi adatulutsa chikwanje ndipo adandikhapa nacho pabondopa. Kaamba ka ululu kuchokera apo sindikumbukanso chomwe chidachitika ndipo ndidangozindikira ndili pabedi kuchipatala ku Queens cha m’ma 4 koloko madzulo,” adatero.

Iye akuti adazindikiranso kuti K4 500 yomwe adamanga pansalu yake palibe.

“Idali ndalama yomwe ndimati ndiwatumizire agogo anga ku Dedza. Agogowa amadaliranso ine akafuna thandizo,” adatero iye.

Chichitikireni cha izi, mayiyu akungobuula ndi ululu kunyumba kwake. Geni sangachitenso, moyo tsopano wasanduka wovuta.

Mneneri wa khonsolo ya Blantyre Anthony Kasunda akuti wangomva za nkhaniyi koma akufufuza kaye ngatidi adali antchito awo amene adachitira chipongwe mayiyu.

“Ndikudabwa chifuma malo amene mayiwa akukamba ife sitifikako. Ndiye zikundidabwitsa kuti zatheka bwanji kuti mayiwa avulazidwe ndi anthu amene akuti ndi akhonsolo ya Blantyre,” adatero Kasunda, amene akuganiza kuti mwina angakhale anthu ena omwe achita izi.

Pamene Kasunda akufufuza, moyo wa Masamba uli pachiswe chifukwa ana ake akudalira iye kuti asake chakudya cha tsiku ndi tsiku komanso zofunikira kusukulu.

“Andiphera tsogolo. Tikadya ndiye kuti ndachita geni. Nawo mpamba udathera kuchipatala. Chochita chikundisowa,” adalira mayiyu pocheza naye kunyumba kwake.

Related Articles

Back to top button