Nkhani

Mbusa amuganizira kugwirira wozelezeka

Apolisi m’boma la Neno akusunga m’chitokosi mbusa wina wa zaka 52 yemwe amatchuka kutyi “Pastor Joshua” wa mpingo wa United of God pomuganizira kuti adagwirira mtsikana wodwala nthenda yakugwa wa zaka 16.

Mbusayo, yemwe dzina lake lenileni ndi Juwayo Antoniyo amachokera m’mudzi mwa Siyali Traditional Authority(T/A) Chapananga m’boma la Chikwawa.

Malinga ndi mneneri wa apolisi m’boma la Neno Raphael Kaliati, Antoniyo adakumana ndi mtsikanayo Lachisanu pa May 5 akuchokera ku chigayo.

“Mtsikanayo adaima panyumba ya mbusayo kupemphako madzi akumwa, ndipo mbusayo adamuuza kuti angolowa n’kukamwera madziwo m’nyumbamo. Apa adamutsatira mtsikanayu ndi kumugwiririra,” adatero Kaliati.

Iye adati mtsikanayo adakamuneneza mbusayo kwa mayi ake omwe adakadandaula kupolisi.

“Kalata yaku chipatala yatsimikiza kuti mtsikanayu adagwiriridwadi,” adatero Kaliati.

Malinga ndi apolisiwa mbusayo aonekera kubwalo la milandu masiku akubwerawa.

Izi zakhumudwitsa mamembala a mpingowu.

Mkucheza kwathu ndi Traditional Authority Mlauli yemwenso ndi mmodzi mwa anthu omwe amapemphera mumpingowo, adati chokhumudwitsa n’choti mtsikanayu amagwa.

Mlauli adati mbusayo adayamba mpingowu m’chaka cha 2014 ndipo anthuwa amamukhulupirira.

“Mbusayotu amaonetsa ngati weniweni m’zochitika zake. Nthawi zina amakafika mpaka ku Tete m’dziko la Mozambique kukalalikira, choncho titamva kuti wagwidwa pokhudzidwa ndi nkhaniyo, tazunguzika,” adatero Mlauli.

Iye adati Antoniyo wabwerera kuchoka ku Mozambique chaka chathachi.

Mlauli adaonjezera kuti m’busayu wasiya anthu opemphera pa mpingowo pa umasiye.

“Ife pakutivutanso ndi poti iyeyu adayambitsa mipingo ku Mulanje komwe iliko iwiri, ku Ndirande mumzinda wa Blantyre, ku  Zomba ndi ku Chikwawa, kodi nkhosa zake m’madera onsewa zitani,” adadandaula motero Mlauli.

Mbusayu ali pa banja. 

Related Articles

Back to top button