Nkhani

MEC igwira njakata pa zisankho zapadera

Zinthu sizikuyenda kubungwe loyendetsa zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) komwe tsogolo la zisankho zapadera silikudziwika.

Lachitatu lapitali, mkulu wa nthambi yoona za chuma kubungweli, Linda Kunje, adauza Tamvani kuti zisankho zachibwereza zichitikabe mtsogolo muno koma tsiku lenileni silikudziwika.

Mathanga: Tikudikirabe ndalama kuchokera kuboma
Mathanga: Tikudikirabe ndalama kuchokera kuboma

Posachedwa bungwe la MEC lidatulutsa chikalata chodziwitsa onse okhudzidwa ndi zisankhozi kuti ayamba aziimitsa kaye kaamba koti boma silidapereke ndalama zoyendetsera zisankhozi, zomwe zikuyembekezeka kuchitika ku Mchinji West Constituency, Kaliyeka Ward ku Lilongwe City South East Constituency, Sadzi Ward ku Zomba Central constituency, Bunda Ward ku Kasungu Central Constituency ndi Bembeke Ward ku Dedza South Constituency.

Mmodzi mwa makomishona kubungweli, Jean Mathanga, akuti pakufunika zosachepera K499 miliyoni zoyendetsera zisankhozi.

Mathanga adati boma silidawapatse ndalamazo koma adatsimikiza kuti zisankhozi zichitikabe mtsogolo muno.

Koma mneneri wa nthambi yoona za chuma kuboma, Nations Msowoya, watsindika kuti boma silipereka ndalama ku MEC pokhapokha lipoti lofotokoza za kusokonezeka kwa ndalama kubungweli litatulutsidwa.

Msowoya: Boma silipereka  msanga  ndalama
Msowoya: Boma silipereka
msanga ndalama

“Ife tidapempha kuti pakhale kafukufuku pa momwe ndalama zidayendera ndipo chomwe tikudikira ndi lipoti. Akatipatsa lipotilo, ndipo tikakhutitsidwa nalo tikhala okonzeka kupereka ndalamazo,” adatero Msowoya.

M’chaka cha 2012 mpaka 2014, kubungweli kudasowa ndalama zoposa K15 miliyoni. Kusowa kwa ndalamazi kudachititsa kuti akuluakulu ena kubungweli akakamizidwe kuti akapume kaye ndi cholinga choti afufuze bwino za mmene ndalama zosowazo zidayendera.

Pa 24 August chaka chino, MEC idatumiza akuluakuluwo, omwe ndi mkulu wa zisankho Willie Kalonga, komanso Harris Potani, George Khaki, Khumbo Phiri, Edington Chilapondwa, Chimwemwe Kamala, ndi Sydney Ndembe kuti abapuma kaye pomwe zofufuzazo zili mkati.

Zitachitika izi, mu August momwemo, boma lidalemba anamnadwa atatu, Rex Harawa, Stevenson Kamphasa ndi Duncan Tambala kuti achite kafukufuku pa kusokonekera kwa ndalamazo.

Koma izi zili chonchi, Kunje akuti zisankho zikhalapobe posakhalitsapa.

“Mitima ya anthu ikhale mmalo. Ngakhale sitingalonjeze tsiku lenileni lomwe zisankhozi zidzachitike, zichitika ndithu posakhalitsa,” adatero iye.

Si izi zokha, kumwaliranso kwa wapampando wa MEC, Maxon Mbendera, ndi komwe kukukayikitsa ngati bungweli lingapangitse zisankho posakhalitsa. Koma malinga ndi Kunje, ili si vuto.

Iye adati: “Palibe chovuta, kupanda iwo ndiye kuti ine ndidzaima kulengeza momwe chisankho chayendera.” n

Related Articles

Back to top button