Nkhani

MESN ikufuna kuwerengera kwapadera

Listen to this article

Mgwirizano wa mabungwe a zachisankho la Malawi Electoral Support Network (Mesn) lati likumenyerera mabungwe ena kuti lidzakhale ndi malo apadera owerengera mavoti pachisankho cha 2014.

Bungweli likufuna malo apaderawa kuti adzafanizire zotsatira za chisankho ndi zimene bungwe loona za chisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) lidzapeze. Izi ndi zothandiza kuti pasakhale chinyengo chobera mavoti poonkhetsa.

M’sabata ikuthayi, Mesn idali ndi msonkhano wofuna kumva maganizo a mabungwe amene adapatsidwa chilolezo ndi MEC poyendetsa nawo chisankho.

Wapampando wa bungweli Steven Duwa adati njirayi ndi yabwino ndipo ingathandize akadaulo amene alibe mbali kuunikira bwino momwe anthu aponyera voti komanso kuwerengera mavotiwo.

Iye adati bungwelo likukonza zodzatumiza akadaulo 84 oona momwe chisankho chikuyendera komanso akadaulo 800 okaonkhetsa mwapadera mavoti komanso anthu ena 1 500 owona chisankho kuti pasakhale chinyengo.

“Tikufuna kugwira ntchitoyi limodzi ndi mabungwe ena kuti pakhale chilinganizo chapadera kuti chisankho chilongosoke,” adatero Duwa.

Ngakhale MEC idavomereza Mesn kuti ikhoza kukhazikitsa chilinganizochi, bungwelo lidati sichidzakhala chanzeru kuti Mesn idzangoonkhetsa mavoti m’madera ochepa. Bungwelo lidati ntchitoyi iyenera kugwiridwa m’madera onse a dziko lino.

Zikuoneka kuti chisankho cha 2014, mpikisano ukhala waukulu, choncho chilinganizochi chikhoza kuthandiza kuthana ndi ziwawa.

Related Articles

Back to top button
Translate »