Chichewa

Milandu mbweee! mu 2016

Listen to this article

Chapita chaka cha 2016 chomwe dziko lino lidaona ina mwa milandu ikuluikulu ikulowa m’mabwalo a milandu ndi kuweruzidwa.
Umodzi mwa milanduyi udali wa yemwe adali nduna ya za chilungamo zaka zapitazo yemwenso ndi kadaulo pa malamulo, Ralph Kasambara.
Kasambara, pamodzi ndi Pika Manondo komanso MacDonald Kumwembe adayankha mlandu woti adakonza chiwembu chofuna kupha mkulu woyendetsa ndondomeko za chuma wakale Paul Mphwiyo mu 2013.

Kasambara (wasuti) kupita kundende

Mwezi wa July, bwalo la milandu lalikulu mumzinda wa Lilongwe lidamupeza Kasambara wolakwa pamlanduwo ndipo mwezi wa August adagamulidwa kukasewenza jere kwa zaka 13.
Manondo ndi Kumwembe adagamulidwa kukasewenza jere zaka 15 ndi 11 aliyense pa milandu iwiri: yochita upo pofuna kupha komanso mlandu wofuna kupha Mphwiyo panja pa nyumba yake ku Area 43 mumzinda wa Lilongwe usiku wa September 13 chaka cha 2013. Milanduyi asewenza paderapadera. Pamodzi, Mandondo ndi Kumwembe asewenza zaka 26.
Mlanduwutu tsopano uli kubwalo la apilo.
M’chakachi tidaonanso ‘fisi’ wa ku Nsanje, Eric Aniva, akukalowa m’chitokosi pogona ndi amayi 104 m’bomali.
Aniva yemwe ndi wa zaka 45, wochokera m’mudzi mwa Tosina kwa mfumu yaikulu Mbenje, m’bomalo adapezeka wolakwa pa milandu iwiri yokhudza kuika miyoyo ya ena pachiswe potsatira miyambo ya makolo.
Aniva adanjatidwa pomwe adauza wailesi ya atolankhani a British Broadcasting Corporation (BBC) za ‘ufisiwu’ mwezi wa July.
Ngakhale Aniva adaukana mlanduwu pa November 22, woweluza milandu Innocent Nebi adamugamula kukasewenza zaka ziwiri ku ndende. Padakali pano, womuyimira Michael Goba Chipeta wachita apilu.
Nawo mlandu wa mtsogoleri wagulu lomenyera ufulu wolanda malo m’maboma a Thyolo ndi Mulanje la Peoples Land Organisation (PLO) Vincent wandale udali mkamwamkamwa mwa anthu m’chakachi.
Bwalo la milandu la Blantyre Magistrate lidapeza Wandale wolakwa pamilandu itatu ndi

Related Articles

Back to top button
Translate »