Milandu yachepa ku Blantyre

 

Milandu yosiyanasiyana mu mzindawa Blantyre yatsika kuchoka pa 328 mu February chaka chatha kufika pa 204 mwezi omwewo chaka chino, atero apolisi.

Wachiwiri kwa mneneri wa polisi mu mzindawo, Dorrah Chathyoka adati iyi ndi nkhani yosangalatsa.

“Kutanthauza kuti milandu yomwe anthu amapalamula yatsika ndi 37.8 pa 100 iliyonse. Iyi ndi nkhani yabwino kutsimikizira ntchito yomwe apolisi a Blantyre akugwira usiku ndi usana,” adatero Chathyoka.

Iye adati polisi yawo idakhazikitsa ndondomeko zothana ndiupandu zomwe zayamba kubala zipatso.

“Mwazina ndikuyendayenda komwe apolisi akuchita m’madera onse. Ena akumavala zovala za polisi ndi ena zovala zawamba kuti tithane ndi upandu,” adatero iye.

“Izitu zikumachitika usiku ndi usana pamene tikumayenda pa galimoto, njinga komanso ena kuyenda wapansi. Takhazikitsanso zipata m’misewu, tikumatola onse amene akuyenda nthawi yosaloledwa popanda chifukwa chenicheni,” adaonjeza Chathyoka.

Iye adati zinanso zomwe achita ndikupanga ubale wabwino pakati pa apolisi ndi anthu okhala mumzinda wa Blantyre.

“Tidakhazikitsa polisi yam’madera, tikulankhulana bwino ndi anthu. Komanso kugawana maganizo ngati pafunika kutero.”

Chathyoka adati kudzera m’njira zotere, apolisi akumanjata owaganizira kupalamula mlandu mosavuta pamene anthu akumawatsina khutu.

Anthu akupemphedwa kuti apitirize kupanga ubale wabwino ndi a polisiwa kuti nkhani yabwinoyi ichitika kwa nthawi yotalikirapo.

“Cholinga ndi kupanga Blantyre wokomera aliyense,” adatero.

Share This Post