Nkhani

Miyambo ya ukwati

Listen to this article

Ukwati sangotengana ngati nkhuku, pali miyambo yake. Ukalakwitsa miyamboyi, mavuto ena akakugwera umasowa mtengo wogwira. Pakati pa Achewa miyambo ya ukwati nayo ilipo. KONDWANI KAMIYALA adacheza ndi Chikumbutso Funani wa m’mudzi mwa Phulusa kwa T/A Kasumbu ku Dedza kuti atambasule zoyenera kutsata. Adacheza motere:

Akulu zikuyenda?

Zikuyenda pang’onopang’ono, mavuto a zachuma omwewa basi.

Funani: Kukagwa maliro ungasowe mtengo wogwira
Funani: Kukagwa maliro ungasowe mtengo wogwira

Ndaona mukuchita izi za kabanza. Chiyambire ntchito ndiyomweyi?

Ayi ndithu. Ndidakagwirako ntchito ku famu ina ku Ntchisi. Ndidagwira kwa chaka chimodzi ndipo nditalandira malipiro anga a pachaka, K47 000, ndidabwerera kumudzi kuno. Ndidagula njinga ndipo ndakhala ndikuchita izi kwa zaka ziwiri.

Maphunziro mudapita nawo patali bwanji?

Ndidalekeza sitandade 7 pasukulu ya Chipaluka. Mudziwa zovuta za kuno kumudzi.

Zovuta zanji?

Makolo ambiri amakakamiza ana awo kuti aleke sukulu azikawathandiza kumunda kapena kupita kuphiri kukasaka nkhuni. Pofuna kuti tisaone kuzunzika kotero, ambiri timasiya sukulu nkukakwatira kapena kukwatiwa kuti tizidzipangira tokha zapakhomo. Ana ena akukwatira ali ndi zaka 15!

Tsono miyambo ya ukwati imayenda bwanji kuno?

Kunotu kumakhala kupereka chapamudzi komanso ya chitengwa. Komanso kuli chiwongo, chamsana chimene madera ena amati malowolo komanso pamakhala nkhuku.

Tafotokozani poyamba za chapamudzi ndi chamsana.

Chapamudzi ndi ndalama zimene zimaperekedwa ngati mwamuna akufuna kukhala mkamwini m’mudzi. Ndalamayi imapita kwa mfumu. Chitengwa ndiye umapereka kwa mfumu pamene ukutenga mkazi m’mudzi kuti ukakhale naye kwanu.

Kodi mitengo yake imasiyana?

Eya imasiyana. Mwachitsanzo, padakali pano chapamudzi ndi K7 000 pomwe ya chitengwa ndi K5 000.

Cholinga choperekera kwa amfumu nchiyani? Iwo chikuwakhudza nchiyani pamene anthu awiri akondana?

Musatero. Kodi utangobwera nkukwatira m’mudzi amfumu osadziwa powapatsa chapamudzi utamwalira mwambo wa maliro ungayende bwanji? Nanga utatenga mkazi kupita naye kwanu amfumu osadziwa chifukwa sunawapatse ya chitengwa, mkaziyo nkumwalira mwambo wa maliro ukhala wotani? Mfumu imakana kuti sitikudziwa kuti tili ndi mkamwini kapena mkazi wakuti ndi nthengwa m’mudzi wina.

Kodi mudachita kupita kwa mfumu kukapereka ndalamayo?

Ayi. Mwa mwambo wake, tidapita kwa eni banja. Pamtundu wa chifumu amasankha munthu mmodzi amene amatchedwa mwini banja. Tikapereka kwa iwo ndiwo amakapereka kwa mfumu.

Tsono munakamba za chiwongo, chamsana komanso nkhuku. Tatambasulani.

Chiwongo chimaperekedwa ngati kuthokoza kuti mkazi adaleledwa mpaka kukula. Dziwani kuti liwu loti chiwongo limatanthauzanso mfunda umene amayi amakhala nawo. Mwachitsanzo, mwana wamkazi wa Obanda chiwongo chake ndi Nabanda. Tikakamba za chamsana kapena malowolo ndiye amaperekedwa kwa mayi a mkazi. Nkhuku ndiye ndi ija amagawana ankhoswe.

Kodi anthu akuzitsatabe?

Alipo ambiri amene akutsata. Koma nthawi zina ena satsatira izi chifukwa mitundu ya sakanikirana.

Related Articles

Back to top button