Nkhani

Miyezi ikutha osalandirandalama za mthandizi

Listen to this article

 

Akugona ndi njala, ena akudya nyanya (mizu ya mitengo yoyanga) pamene akudikirirabe ndalama zawo za ntchito ya mthandizi yomwe zatenga nthawi.

Tamvani yapeza kuti maboma ena, anthu atha miyezi iwiri asadalandirebe ndalama zawo chigwirireni ntchito mu November pamene maboma ena alandira kumene.

Kusowa kwa ndalama zogulira ufa kwadzetsa kudya nyanya
Kusowa kwa ndalama zogulira ufa kwadzetsa kudya nyanya

Koma mneneri wa nthambi yoyendetsa ndondomekoyi ya Local Development Fund (LDF) Ina Thombozi wati chomwe akudziwa nchakuti ndalamazi zidatumizidwa m’maboma kuti anthu alandire ndiye oyenera kulankhulapo ndi amene akuyendetsa ndondomekoyi paboma.

Kuchedwa kwa ndalamazi kwachititsa kuti anthu ayambe kudya mizu ya nthochi pamene ena akudya nyanya zomwe ena zikuwatupitsa kapena kutsekula m’mimba.

Boma lidakhazikitsa ndondomekoyi kuti ithandize anthu ovutika. Anthuwa amalandira K600 patsiku akalima msewu koma ndalamazo amayenera kulandira pakadutsa masiku 12 chiyambireni kulimako.

Kumayambiriro a January, nthambi ya LDF idatulutsa uthenga kuti ndalama zokwanira K5.4 biliyoni zatumizidwa m’makhonsolo onse kuti anthu ayambe kugwira ntchitoyi ndipo anthu 450 000 okha ndiwo apindule ndi thandizoli m’dziko lonse.

Monga akufotokozera gulupu Mpochela wa kwa T/A Phambala m’boma la Ntcheu, anthu ake atha miyezi iwiri asadalandire ndalamazo chilimireni msewu.

“Adayamba kalekale kulengeza za tsiku lomwe tilandire ndalamazo. Tidayambatu kulima mu November koma mpaka lero sitidalandire ndalama,” adatero Mpochela.

M’mudzi mwa Mpochela tsopano muli nkhawa kuti wina angamwalire ndi njala chifukwa anthu akusowa chakudya.

Charles Chinangwa wa mwa gulupu Mpochela m’bomalo amene ali ndi ana 8 akuti akugonera nyanya kapena mizu ya nthochi pamene alibe pothawira.

Pocheza ndi Tamvani uko mphika wa nyanya uli pamoto, Chinangwa adati boma liwapatse ndalama zawo kuti agulire chakudya.

“Takhala tikudya nyanya kuyambira mu October chaka chatha. Panopanso nyanya zikusowa ndipo sitikudziwa kuti tilowera kuti. Ena osemphana nazo magazi akutupa nazo pamene ena zikuwatsegula m’mimba,” adatero Chinangwa.

Gulupu Mpochela akuti wakhala akupita ku ofesi ya DC m’boma lawo koma palibe thandizo lomwe alandira kufika pano.

“Ndidakafikanso kwa phungu wathu, akungoti apereka dandauloli ku boma koma kuli ziii, anthu anga akuvutika ndi njala moti ena ayamba kutupa, chakudya kulibe koma anthu adagwira kale ntchito ya mthandizi,” adatero Mpochela.

Yemwe amayendetsa za mthandizi m’bomalo Kondwani Mjumira wati anthu ena sadalandire monga kwa Phambala ndi madera ena koma anthuwa alandira posakhalitsa.

“Ndalama zilipo, ena alandira kale moti kumene mukukunenako akulandira sabata imeneyi,” adatero pamene adatinso akuyenera kufufuza ngati anthu ena sadalandire ndalama kuyambira November.

Maboma ena monga Neno, Phalombe, Mulanje, Thyolo ndi Nsanje anthu akuti sadalandire ndalama zawo pamene ena.

Related Articles

Back to top button
Translate »